top of page
Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa. Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo – Mateyu 7.17 ndi 20
Cikhulupiriro copanda nchito ciri cakufa – Yakobo 2.26b
Pamene tiyang’anira potizungulira tiona cilengedwe cokongola ca Mulungu. Mulungu analenga mitengo yosiyanasiyana. Mitengo ina ibereka zipatso zimene tingadye. Ngati mtengo ndi woipa, udzabala zipatso zoipa. Ngati mtengo ndi wabwino udzabala zipatso zabwino.
Ici ndi cimodzimodzi ca ife anthu. Ngati ciyambi ca miyoyo yathu ndi cabwino, tidzabala zipatso zabwino. Ngati ciyambico ndi coipa, tidzabala zipatso zoipa. Tiyeni tiganizireko zipatso za m’miyoyo yathu.
Ciyambi ca zipatso zathu
Mulungu analenga Adamu ndi Hava; anthu oyamba a pa dziko lapansi[1]. Nthawi zonse Adamu ndi Hava anatamanda ndi kulemekeza Mulungu ndi mau ao, makhalidwe ao ndi maganizo ao. Miyoyo yao inakondweretsa Mulungu: iwo anabala zipatso zabwino, monga cikondi, cimwemwe, mtendere, cifundo ndi cikhulupiriro[2]. Anacita tero pakuti ciyambi ca miyoyo yao (mitima yao) cinali cabwino[3]. Anali olumikizidwa ndi Mulungu yekha.
Koma tsiku lina Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu[4]. Zonse zasinthika. M’malo mwa kukhala ndi mitima yabwino, tsono anthu abadwa ndi mitima yoipa yobala zipatso zoipa[5]. Zipatsozi zoipa zichedwa macimo. Ticimwa cifukwa ca mitima yathu yoipa. Macimo asakondweretsa Mulungu[6]. Kuli macimo ambiri, mwacitsanzo codetsa, mkwiyo, nsanje, mipatuko, kupembedza mafano, dama, ciphuphu, cipongwe ndi cisiriro[7]. Cifukwa ca mitima yathu yoipa, mbadwidwe wa miyoyo yathu ndi kotero kuti tidzikonda m’malo mwa kukonda Mulungu[8]. Sitikhoza kukhala moyenera pa maso pa Mulungu ndi kukhala pafupi naye, komabe tikayeretsedwa ku macimo athu[9].
Umoyo wa Paulo
M’Afilipi 3.6 Paulo analemba kuti anali ndi cangu ca kwa Mulungu. Ankacita zonse zotheka kuti asangalatse Mulungu[10]. Anaphunzitsidwa za Mulungu ndipo anadziwa zambiri zoposa anthu ena. Anali waluntha ndipo anasunga konse malamulo a Mulungu. Anthu ena sanapeze colakwa ciriconse m'moyo mwake. Paulo ankaganiza kuti anabala zipatso zabwino. Pamene anaona anthu ena kubala zipatso zoipa kulingana ndi iye, Paulo anacita zatheka kuwaleketsa.
Tsiku lina pamene Paulo anali pa ulendo, Yesu Mwana wa Mulungu anadzibvumbulutsa kwa iye[11]. Kuyambira nthawi iyo, Paulo anaphunzitsidwa ndi Mulungu. Mulungu anamphunzitsa kuti si cotheka kubala zipatso zabwino ngati Yesu akalibe kupangitsa mitima yathu kukhala yabwino[12]. Paulo anaphunzira kuti kulondola malamulo kapena kucita zabwino sizikhoza kuthetsa bvuto la macimo amene atilekanitsa ndi Mulungu[13].
Mwina muganiza cimodzimodzi monga Paulo ankaganiza. Kapena muganiza kuti Mulungu adzakulolani kukhala Kumwamba pakuti mumatengako mbali ku calichi ndipo mumacita zatheka. Kapena muganiza kuti Mulungu adzakulandirani, pakuti mucimwa mocepa kusiyana ndi anthu ena. Mwina muganiza kuti mtima wanu unasinthidwa pamene munaleka kumwa mowa kapena kucita cigololo. Koma msintho m’miyoyo yathu sitanthauza mtima wosinthika mopanda bvuto. Ganizirani birimankhwe: angakhale kusintha mtundu wake, ali yomweyo. Tiyenera kukonzedwanso konse mwatsopano tisanakhale abwino pa maso pa Mulungu ndiponso tisanakhoze kubala zipatso zabwino zomkondweretsa Mulungu[14]. Liu lina la m’Baibulo limene litanthauza kukonzedwanso konse mwatsopano ndilo ‘mtima watsopano’ kapena ‘kubadwa mwatsopano’.
Yesu, wopatsa mitima yatsopano
Mulungu afuna anthu kulandira mtima watsopano wocokera kwa Iye. Anapanga njira yapadera kuti anthu apulumutsidwe[15].
Yesu Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lapansi[16]. Anakhala moyo woyenerera. Sanabale zipatso zoipa: sanacimwe. Mtima wake unali wabwino, pakuti Iye ndi Mwana wa Mulungu. Koma anthu sanakonde Yesu pa kuwaphunzitsa za mitima yao yocimwa ndiponso za cofunikira cao ca kukhululukidwa[17]. Iwo anamkhomera pa mtanda ndipo Yesu anafa[18]. Koma patapita masiku atatu Yesu anauka kwa akufa[19]. Iye ali ndi mphamvu zonse ndipo ali wamoyo!
Baibulo litiuza momveka bwino kuti nchito zathu sizikhoza kutiyanjanitsa ndi Mulungu, koma Yesu akhoza[20]! Lekani kuyesa kubala zipatso zabwino mwa mphamvu yanu ngati mtengo (mtima wanu) akadali woipa. M’malo mwa ici, dzicepetseni. Uzani Mulungu za zipatso zoipa za m’moyo mwanu (=ululani macimo anu)[21]. Siyani macimo anu ndipo yang’anirani kwa Yesu yekha kukupulumutsani ku macimo anu (=lapani)[22]. Bvomerezani zimene Mulungu akamba za uchimo wanu ndipo dziperekeni kwa Iye (=khulupirirani)[23]. Mwa cisomo Iye adzakulandirani, pakuti Iye ndi wabwino ndi wacisomo[24].
Yesu anafa nauka kwa akufa kuti ife tilandire cikhululukiro ndi mitima yatsopano yolamuliridwa ndi Iye[25]. Anthu onse amene agonjera kusintha mitima yao, koma apereka mitima yao yocimwa kwa Yesu, ndiwo olungama pa maso pa Mulungu.
Ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu – Aroma 3.24
Yesu akonzanso mwatsopano anthu ake. Iwo adzabala zipatso zabwino zocokera m’mitima yokonzedwa bwino ndi Yesu[26].
Zipatso zabwino ziri zofunikira
Zipatso zabwino ndizo zotulukamo za kukhazikika mwa Yesu[27]. Yesu ananena kuti aliyense amene akhala mwa Iye, abala zipatso zambiri[28]. Munthu amene saonetsa zipatso zabwino, sapezeka mwa Yesu. Baibulo likamba kuti cikhulupiriro ca munthu wotere ciri cakufa[29]. Zipatso zabwino ziri zofunikira pa nkhani ya cikhulupiriro.
Anthu a Mulungu apemphera, afalitsa Uthenga Wabwino, akonda ndi kukhulupirira Mulungu, adziletsa ku macimo, akondana ndi kumvera Mulungu ndi zina zambiri. Inde, anthu a Mulungu angacimwe, koma akazindikira kuti acimwa, iwo amva cisoni ndipo kuulula macimo ao kwa Mulungu kumpempha cikhululukiro.
Anthu a Mulungu aphunzira kubala zipatso zina. Kupyolera mwa Baibulo ndi zocitika zosiyanasiyana Mulungu awaphunzitsa kusanduka mofanana ndi Yesu komanso kulemekeza Mulungu[30]. Liu lina limene Baibulo ligwiritsa nchito kufotokozera za ici ndilo ‘kusadza’[31]. Liu lina la kuphunzira kukhala momwe Mulungu afuna ndilo ‘kuyeretsedwa’[32]. Kukhala woyera ndi kofunikira pakuti kopanda ciyeretso kulibe munthu amene angakhale pafupi ndi Mulungu woyera[33].
Ciweruzo ca Mulungu
M’Aroma 2.5 ndi 6 tiwerenga kuti Mulungu adzatibwezera kulingana ndi nchito zathu; adzatibwezera kulingana ndi zipatso zathu. Ngati mitima yathu siyisinthidwa m’miyoyo yathu ndipo ibalabe zipatso zoipa, tidzakhala m’Gehena muyaya[34]. Ngati mtima wanu ndi woipa, lapani ndipo khulupirirani Ambuye Yesu.
Ngati Yesu anasintha mtima wanu ndipo m’moyo wanu muli zipatso zabwino, thokozani Mulungu pa zimene acita kwa inu ndi mwa inu. Osaiwala kuti moyo wanu usiyana ndi wa anthu ena mwa cisomo. Yamikirani Mulungu mosaleka ndipo khalani moyo wanu wakubala zipatsa zabwino ku ulemerero wake[35]. Tsiku lina pamene moyo wanu watha, Mulungu adzakutengani kukhala naye Kumwamba[36].
~
Kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu nchito yonse yabwino, ndi kukula m’cizindikiritso ca Mulungu – Akolose 1.10
----------------------------
[1] Genesis 1 ndi 2, [2] Agalatiya 5.22, [3] Mateyu 12.35, [4] Genesis 3, [5] Yobu 15.14, Salimo 51.5, Salimo 14.1-3, Marko 7.21-23, Miyambi 20.9, Yesaya 66.4, [6] Akolose 1.21, [7] Agalatiya 5.19-21, [8] Aefeso 2.3, Aroma 8.5 ndi 7, Genesis 6.5, Yohane 3.3, [9] Tito 2.14, Yesaya 57.17, Ezekieli 39.24, [10] Afilipi 3.4-6, [11] Macitidwe 9, [12] Akolose 1.6, Afilipi 1.11, [13] Aroma 3.28, Agalatiya 2.16, [14] Yohane 3.7, Ezekieli 36.26 ndi 27, 2 Akorinto 5.17, [15] Aroma 5.6-8, [16] Luka 2, [17] Yohane 6, [18] Mateyu 27, [19] Mateyu 28, [20] 1 Yohane 2.2, [21] 1 Yohane 1.9, [22] Ezekieli 18.32, [23] Aroma 4.5, [24] Aroma 3.22-24, [25] Agalatiya 2.20, Akolose 2.11-14, Aefeso 2.5, [26] Aefeso 2.10, Yohane 15.18, [27] Tito 2.14, [28] Yohane 15.5, [29] Yakobo 2.26, [30] Aroma 5.3-5, Akolose 1.10, [31] Yohane 15.2, [32] Aefeso 5.26 ndi 27, Tito 2.14, [33] Ahebri 12.14, [34] Mateyu 15.13, Yohane 15.6, [35] Afilipi 1.11, Yohane 15.8, 1 Akorinto 6.20, [36] Cibvumbulutso 22.14
bottom of page