BAIBULO
Baibulo
Ndilo Buku langa
Ndikonda Mau a Mulungu
Baibulo
CITANI ZONSE
1 Akorinto 10.31
Citani zonse ku ulemerero, wa Mulungu (2x)
Wa Mulungu (2x)
Citani zonse ku ulemerero, wa Mulungu
Konda mnzako monga udzikonda wekha, ati Mulungu (2x)
Ati Mulungu (2x)
Konda mnzako monga udzikonda wekha, ati Mulungu
This is my commandment that you love one another, that your joy may be full (2x)
That your joy may be full (2x)
This is my commandment that you love one another, that your joy may be full
CIYEMBE-
KEZO CANGACO
Ciyembekezo cangaco
Camangidwa pa mwaziwo;
Sindikhulupira pena,
Ndingotsamira pa Yesu
Ndaima nji pa Kristuyo,
Ndiye Cithanthwe colimba,
Maziko ena mpa mcenga.
Ndaima nji pa Kristuyo,
Ndiye Cithanthwe colimba,
Mziko ena mpa mcenga.
COLIMBITSA MTIMA NDI
Colimbitsa mtima ndi, Conditsogolera, M'njira ya Mulunguyo, Ine ndili naco
M'Bukuli ine ndi, Onse owerenga, Mau a Mulunguwo, Timapeza moyo.
Zinthu za kumundazo, Zilimbitsa thupi; Zolembedwa m'Bukumo, Zimadyetsa mtima.
Ndikacimwa Bukuli, Lindiyambotsutsa; Limanditonthoza ndi, Mau a mtendere.
Pakudera nkhawa 'ne, Pakucita mantha, N'kawerenga m'Bukuli, Lindipatsa mphamvu.
Lindionetsera 'ne, Cifuniro cake, Ca Mbuyanga Yesuyo, Ndikamvere bwino.
Zonse mwazilembamo, Mzimu Wakuyera, Kuzimvera zonsezo, Mundithangatire
M'Buku lakuyerali, Powerenga ife, Mbuye mutipatsemo, moyo moyo moyo
COMBO CA NOWA
Genesis 6-8
Combo ca Nowa cinayandama
(combo ca Nowa)
Combo ca Nowa cinayandama
(combo ca Nowa)
Combo ca Nowa
(combo ca Nowa)
Combo ca Nowa cinayandama
(combo ca Nowa)
Combo ca Nowa
(combo ca Nowa)
Combo ca Nowa cinayandama
FUNANI YEHOVA
Funani Yehova popezeka Iye (2x)
Itanani Iye pamene ali pafupi (2x)
Yesaya 55.6
Yesaya 55.6
KALE M'MZINDA
Kale m'mzinda wacifumu
Munalimo m'kholamo.
Momwe mkazi anaika
Mwana wake m'ndyeromo.
Ndiye mkaziyo Mariya
Yesu Kristu Mwanayo
Uyu 'natsikira kuno,
Mlungu Mbuye wathuyo.
Anabadwa uyu m'khola
Anagona m'ndyeromo.
Mwa osowa ndi oipa,
Yesu anakhalamo.
KONZEKA, MBALE WANGA
Konzeka, mbale wanga (2x).
Konzeka, mbale wanga, konzeka.
(mbale wanga) Konzeka, mbale wanga, konzeka.
(Yesu) Yesu ndiye adziwa.
Pa Sondo, mwina adzabwera pa Monday.
Monday, mwina adzabwera pa ciwiri.
Pa ciriwi, mwina adzabwera pa citatu.
(Yesu) Yesu ndiye adziwa.
Pa citatu, mwina adzabwera pa cinai.
Pa cinai, mwina adzabwera pa cisanu.
Pa cisanu, mwina adzabwera pa ciweru.
(Yesu) Yesu ndiye adziwa.
Pa ciweru, mwina adzabwera pa Sondo.
Pa Sondo, mwina adzabwera pa Monday.
Pa Monday, mwina adzabwera pa ciwiri.
(Yesu) Yesu ndiye adziwa.
KUOPA YEHOVA
Kuopa Yehova ndiko, ciyambi ca kudziwa (2x)
Kudziwa, kudziwa, ciyambi ca kudziwa (2x)
Kuopa Yehova ndiko, kudana ndi coipa (2x)
Coipa, coipa, kudana ndi coipa (2x)
Miyambi 1.7
LOLANI ANA
Lolani ana adze kwa Ine
ndipo musawaletse
Pakuti Ufumu wa Mulungu
uli wa otere (2x)
Luka 18.16
MBUSA WABWINO
Ine ndine Mbusa Wabwino
Mbusa Wabwino
Ataya moyo wace, cifukwa ca nkhosa
Ine ndine, Mbusa Wabwino, Mbusa Wabwino
Ataya moyo wace, cifukwa ca nkhosa
Yohane 10.11
MONGA ATATE ACITIRA
Monga Atate acitira
ana ace cifundo,
Yehova acitira cifundo
iwo akumuopa Iye.
Lemekezani Yehova (2x)
Yehova acitira cifundo
iwo akumuopa Iye.
Salimo 103.13 ndi 21
MUTHANGE MWAFUNA
Mateyu 6.33
Muthange mwafuna Ufumu wace
Ndi cilungamo cace,
Ndipo zonse zimenezo
Zidzaonjezedwa kwa inu
Aleluya (3)
Alelu - Aleluya
Seek ye first the Kingdom of God,
and his righteousness;
and all these things shall be added unto you
Allelu - alleluia
Alleluia (3x)
Allelu- alleluja
NDIKWEZA MASO
Ndikweza maso anga ku mapiri
Thandizo langa lidzera kwa Yehova
Thandizo langa, thandizo langa
Thandizo langa lidzera kwa Yehova
Salimo 121.1 ndi 2a
NDIPEREKA MOYOWU
Ndipereka moyowu
Kwa Ambuye wanga ‘Nu;
Manja ‘wa acitetu
Cifuniro canuco
Cifuniro cangaci
Cikhaletu canunso;
Ndipereka mtimanga
Ukhaletu wanunso.
Ndipereka cikondi
Pa mapazi anuwo;
Munditenge ndense ‘ne
Ndikaletu wanuyo.
NDIPO KUDZALI
Yoweli 3.32
Ndipo kudzali
Kuti yense amene akaitana
Dzina l'Ambuye
Adzapulumutsidwe (2x)
Amene akaitana
Dzina la Ambuye
Adzapulumutsidwe (2x)
Amene akaitana dzina la Ambuye
Adzapulumutdiwe (2x)
ONA MU MTIMA
Oona mu mtima, dzani mokondwera,
Tiyeni, tiyeni ku Betelehemu;
Modyera ng’ombe muli Mfumu yathu.
Tiyeni timgwadire, tiyeni timgwadire,
Tiyeni timgwadire, Kristuyo.
Angelo kwezani nyimbo zanu zonse,
Mwambamo mumveke zoyamikazo,
Lemekezani Mlungu Wakumwamba.
Tiyeni timgwadire, Tiyeni timgwadire,
Tiyeni timgwadire, Kristuyo.
PACIYAMBI MULUNGU ANALENGA
1. Paciyambi Mulungu analenga
Kumwamba ndi dziko lapansi.
Iye analenga zonse zabwino.
Yehova ndiye Mlengi wathu.
Yehova Mulungu, atipatsa thandizo ndithu.
Thandizo licokera kwa Mulungu.
Atipatsa thandizo ndithu.
2. Tsiku lina zonse zinaipadi.
Kaamba ka kusamvera Mlungu.
Mwa cisomo Yesu anapatsidwa
Kuferathu anthu ocimwa.
Yehova Mulungu, atipatsa thandizo ndithu
Thandizo licokera kwa Mulungu
Atipatsa thandizo ndithu.
PEMPHA PEMPHA MOYO
Pempha pempha moyo (3x)
Moyo wosatha
Udzaupeza
Ngati upemphera
Masiku onse pemphera
PEMPHERA NTHAWI YA MAMAWA
Pemphera nthawi ya mamawa
Pemphera nthawi ya masana
Pemphera nthawi ya madzulo
Konzeka m'mtima
(Ambuye adziwa)
Adziwa nthawi ya mamawa
Adziwa nthawi ya masana
Adziwa nthawi ya madzulo
Konzeka m'mtima
(Ambuye amamva)
Amamva nthawi ya mamawa
Amamva dziwa nthawi ya masana
Amamva nthawi ya madzulo
Konzeka m'mtima
POYENDA NDI MBUYE
Poyenda ndi Mbuye
Mukuwala kwaceko
Aunikira m'njira mwathu
Pakugwira nchito
Amakhala nafe
Khulupira ndi kumveratu
Khulupira, palibenso njira
Yakukondwa mwa Yesu
Koma kumveratu
SANKHA YAKO
Sankha yako (2x)
Pali njira ziwiri
Sankhayako (2x)
pali njira ziwiri
Ina ipita ku Mwamba
Ina yopita ku moto
Sankhayako (2x)
pali njira ziwiri
TIYENI TIPEMBEDZE
Tiyeni tipembedze
Tiwerame, tiwerame
Tigwade pa maso pa Yehova
Amene anatilenga
Yesu anauka ndithu (2x)
Aleluya, aleluya,
Yesu anauka kwa akufa
ULEMERERO KWA MULUNGU
Ulemerero kwa Mulungu (2x)
Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba
Ndi mtendere pansi pano (2x)
mwa anthu amene akondwera nao.
Luka 2.14
WODALA MUNTHU AMENE
Wodala munthu amene
Akhala naye Mulungu;
Kuti amthandize;
Analenga zakumwamba;
Ndi dziko lapansi;
Ndiye wakusunga;
Coonadi cosatha.
Salimo 146.5 ndi 6
YANG'ANANI KWA INE
Yesaya 45.22
Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe
Yanganani kwa Ine, Yehova
Ine ndine Mulungu palibe wina
Ine ndine Mulungu yekha
Onse, onse, a dziko yang'anani
Yang'anani kwa Ine mupulumutsidwe
Ine ndine Mulungu Yekha
(3x)
YESU KRISTU ALI YEMWEYO
Ahebri 13.2
Salimo 62.2
Yesu Kristu ali yemweyo.
Dzulo, lero, nthawi zonse.
Yesu Kristu ali yemweyo.
Dzulo, lero, nthawi zonse.
Dzulo, lero, nthawi zonse.
M'lungu Yekhayo ndiye thanthwe langa
Cipulumutso canga, msanje wanga.
M'lungu Yekhayo ndiye thanthwe langa.
Sindidzagwedezeka.
Sindidzagwedezeka.
YESU YESU NDI CITSIME
Yesu Yesu ndi citsime ca moyo (2x)
Mkuunika kwanu tidzaona
Kuunika
Yesu Yesu ndi madzi a moyo (2x)
Madzi otumphukira ku moyo
Wosatha
Salimo 36.9
ZINTHU ZONSE
Zinthu zonse, zinthu zonse
Zitheka, zithekha
Ndi Mulungu
Marko 10.27b