top of page
Musatengedwe.jpg

MUSATENGEDWE
NDI MAPHUNZITSO

Kodi Baibulo likamba ciani za atsogoleri a mipingo ndi ziphunzitso zao?


Wacibwana akhulupirira mau onse; koma wocenjera asamalira mayendedwe ace – Miyambi 14.15

Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundu mitundu, ndi acilendo – Ahebri 13.9


Kodi ndi ciani cimene cicitika ngati mukudya cakudya cosasa? Kapena ngati mwamwa cakumwa coipitsitsa? Mudzasoweka ndi kukhala odwala. Anthu anzeru sacita dala cimene cingawaononge. Anthu anzeru samvera ciphunzitso cimene cingawaononge. Baibulo ikamba kuti ciphunzitso cina ndi colamitsa koma cina siciri colamitsa[1]. Ciphunzitso conama ciononga miyoyo yathu yauzimu, monga cakudya cosasa ciononga umoyo wabwino. 

Mulungu atilangiza kukhala osamala pa kumvera ciani komanso pa kumvera yani[2].

Yang’anirani asasokeretse inu munthu (…) Cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa – Mateyu 24.4 ndi 24a

Anthuwa onama amene Yesu analankhulira, anaweruzidwa anthu a Mulungu. Ziphunzitso zao zingamveke bwino. Acita zodabwitsa. Angalemekezedwe ndi kuchedwa azibusa, aneneri, atate, mabishopo, atumwi kapena maina ena otere. Anthu onama angaoneke oona ndi osanamizira.

Yesu atilangiza kusakhulupirira wina aliyense wonena kuti alankhula m’malo mwa Mulungu[3]. Tinganamizidwe ndi ena a iwo. Tiyenera kuyesa aliyense ndi ciphunzitso ciriconse kudziwa ngati zicokera kwa Mulungu. Tiyenera kudziwa kusiyana pa ciphunzitso coona ndi conama. Ngati timvera ciphunzitso colamitsa cabe, tidzakhala athanzi ndi amphamvu m’uzimu.


Mafunso anai

Tiyenera kufunsa mafunso anai kusiyanitsa aneneri ndi azibusa oona ndi onama ndi ziphunzitso zao.

  1. Funso loyamba ndi lakuti, ‘Kodi abusa/aneneri ndi ziphunzitso zigwirizana ndi zimene Mulungu anabvumbulutsa m’Baibulo?’ Ciphunzitso ciriconse cotsutsa ndi Baibulo ciyenera kukanidwa[4]. Ngati wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa – Agalatiya 1.9. Cifukwa cace tiyenera kudziwa zimene Mulungu atiphunzitsa m’Baibulo! Werengani Baibulo masiku onse ndipo pemphani Mulungu thandizo kumvetsa. Baibulo itiuza kuti Mulungu analenga bwino zonse[5]. Koma anthu anasankha kusamvera Mulungu (ndiko kucimwa)[6]. Cifukwa cace ndife olekanidwa ndi Mulungu[7]. Mwa cisomo Mulungu anapereka Yesu, Mwana wake wobadwa yekha, kukonzanso zimene zinaonongedwa[8]. Aliyense wolapa macimo ndi kukhulupirira Yesu yekha pa cipulumutso, alandira umoyo wauzimu wocokera kwa Mulungu ndipo munthuyo ndiye mwana wa Mulungu[9]. Ana a Mulungu alandira cikhululukiro ca macimo ao[10]. Mulungu Mzimu Woyera akhala mwa iwo kuwatsogolera ndi kuwaphunzitsa kulemekeza Mulungu[11]. Iwo adzakhala ndi Mulungu Kumwamba muyayaya[12]. Iwo amene sanalandire cikhululukiro asanafe, adzakhala ku Gehena muyayaya[13]. Gehena ndi malo oipa kwambiri. Uthenga waukulu wa m’Baibulo ndiwo m’mene Mulungu aliri kwa anthu ocimwa. Cifukwa cace aneneneri oona sadzadzilankhulira, koma adzalankhula kwa ulemerero wa Mulungu[14]. Udindo wa mneneri ndiwo kubwezera anthu ocimwa kwa Mulungu mwa kulapa ndi kukhulupirira Yesu[15]. Yesani uthenga umene mumamva ku calichi, pa wailesi ndi pa TV. Kodi Mulungu ndiye pakatikati pa uthenga?

  2. Funso laciwiri ndi lakuti, ‘Kodi munthu wophunzitsa aliri monga za m’Baibulo?’ Baibulo itiuza kuti tikhoza kudziwitsa Akristu onama mwa zipatso zao[16]. Mulungu afuna Akristu kukhala ndi cikhalidwe cabwino coposa, makamaka atsogoleri monga azibusa ndi aneneri[17]. (…) wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa, wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma – 1 Timoteo 3.2 ndi 3. Ganizirani azibusa ndi aneneri amene mudziwa. Kodi ndiwo oyera, odzicepetsa, abwino, olungama, odekha, acikondi ndi odziletsa?

  3. Funso lacitatu ndi lakuti, ‘Kodi ulosi wao ucitikadi?’ Azibusa ndi aneneri onama anena kuti akhoza kunenera za kutsogolo m’dzina la Mulungu ndi ulamuliro wake. Ngati ulosiwo sucitika ndiko cizindikiro cakuti munthuyo ndiye mbusa/mneneri wonama amene angonena zimene anthu akonda kumva[18]. Mneneri akanena m’dzina la Yehova, koma mau adanenawa sacitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanena; mneneriyo ananena modzikuza – Deuteronomo 18.22a. 

  4. Funso lotsiriza ndi lakuti, ‘Kodi munthuyo aphunzitsa ndi kukhala pa zoona?’ Ena a azibusa ndi aneneri alemba mabuku amene asunga nkhani za mabodza. Mulungu alangiza pa izi[19]. Ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe – 2 Timoteo 4.4. Mulungu atiuza kuphunzitsa coonadi: zoona zimene zinacitikadi ndipo zinasonyezedwa zoona, makamaka zoona zimene Yesu anacita[20]. Pakuti sitinatsata miyambi yacabe (…) koma tinapenya m’maso ukulu wace – 2 Petro 1.16


Mathero

Tingazindikire munthu kukhala mneneri, mphunzitsi wa za m’Baibulo, mbusa kapena ciriconse cimene mungache munthu wotero, ngati mafunso awa anai ayankhidwa ndi ‘inde’. Yesani atsogoleri anu a za uzimu. Malizitsani. Londolani zabwino.


Thanzi ndi kupindula m’Baibulo

Nthawi zambiri azibusa, aneneri, mabishopo ndi ena amene aphunzitsa mokhulupirika Baibulo, ali ndi otsatira ocepa cabe. Uthenga wabwino wokhudza macimo ndi cipulumutso mwa Yesu[21]. Koma anthu ena aphunzitsa kuti Utenga Wabwino ukhudza Mulungu wofuna anthu ake kukhala opambana ndi olemera nthawi zonse, monga Abrahamu ndi Solomo m’Baibulo. Tiyese ciphunzitso ici mozindikira za m’Baibulo.

1. Anthu okhulupirira osauka m’Baibulo

Baibulo itilangiza kuti cuma cingatilepheretsa mu za uzimu[22].

Ha! Nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu! – Luka 18.24b

Baibulo itiuza za okhulupirira osauka ndi obvutika. Mkazi wamasiye wosauka analemekezedwa ndi Yesu[23]. Lazaro wopemphapempha analowa Kumwamba koma wacuma sanalowe[24]. Stefano anaphedwa cifukwa ca Yesu[25]. Mose anasiya cuma kukamvera Mulungu[26]. Paulo anamva njala nazunzika[27]. Ngakhale Yesu anasauka[28]. Baibulo siwaikira mlandu cifukwa ca kukhala osauka. Komatu iphunzitsa kuti iwo anakhala naco cuma ca kwa Mulungu[29]. Ici citanthauza kuti analandira moyo wosatha. Njira imene iwo anayankha mabvuto ao itiphunzitsa kukhala odzipereka[30]. Si kuti nthawi zonse tingalemere kapena kusauka cifukwa ca m’mene mgwirizano wathu ndi Mulungu uliri.


2. Kubvutika ndiko mbali ya kukhala Mkristu[31]

M’kati mwa mabvuto Mulungu atithandiza, atisunga, atikonza ndi kutiphunzitsa kudalira pa Iye[32].

M’dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi

Ine – Yohane 16.33

Nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m’cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m’ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri – Macitidwe a Atumwi 14.22


3. Colinga cathu ndi kulemekeza Mulungu

Colinga ca miyoyo yathu ndico kulemekeza Mulungu mwa kufanana ndi Iye mwa Yesu Mpulumutsi[33]. Kufanana naye ndi komwe tiziyang’anirako osati kuyesetsa cuma. Osakhala kudzikonda, koma Mulungu akhale m’kati mwa miyoyo yathu.

Makani opanda pace a anthu oipsika nzeru ndi ocotseka coonadi, akuyesa kuti cipembedzo cipindulitsa – 1 Timoteo 6.5

Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama – 1 Timoteo 6.10a

Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi – Mateyu 6.19a

4. Yesu yekha ndiye Mkhalapakati

Kulibe anthu amene ali ndi mpata wolowa pafupi ndi Mulungu kuposa anthu ena. Mkristu aliyense aloledwa kupemphera molimbika mwa Yesu Mkhalapakati yekha[34]. Tingapemphe anthu ena kutipempherera koma sitidalira pa iwo kutilumikizitsa ndi Mulungu.

Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu – 1 Timoteo 2.5

Yesu agwirizanitsa kwaulere. Ndiko mphatso[35]. Tiyenera kuthandiza atsogoleri a za uzimu okhulupirika[36], koma nthawi zambiri atsogoleri oganizira kwambiri malipiro ndiwo olabadira zinthu zao zathupi. 


5. Tiyenera kuwerenga ndime za m’Baibulo ndi mau anzao

Ndi colakalakika kwambiri kufotokoza ndime ya m’Baibulo ndi kuigwiritsa nchito mwa kumvetsetsa kwathu ndi ku ubwino wathu. Koma ngati tifuna kudziwa zimene Mulungu atiuza, tiyenera kuwerenga Baibulo mwaubwino, mwacitsanzo mwa kuwerenga ndime patsogolo pa ndimeyo ndiponso ndime yotsatirapo. Zitsanzo zina:

  • Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino – Aroma 8.28a. Pamene tiwerenga ndimeyi yokambira ubwino tingaganize kuti Mulungu afuna anthu ake kutukuka nthawi zonse. Koma ngati tiwerenga ndime yotsatira m’mutu umenewo, tipeza kuti Mulungu akamba za ubwino wa anthu kusandulika kufanana ndi Yesu. M’cocitika ciriconse momwe iwo angapezekemo, Mulungu apanga anthu ake kuti akhala monga Yesu[37].

  • Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera – 3 Yohane 1.2. Anthu ena agwiritsa nchito ndime iyi kusonyeza kuti kupindula ndi umoyo wabwino ndizo ufulu wa Mkristu aliyense. Koma ngati muwerenga mwaubwino mudzapeza kuti ndimeyi ndiyo pemphero (ndipemphera). Yankho iri ya kwa Mulungu[38]. Iye ndiye wopambana: asankha kucita ciani[39]. Timkhulupirira kuti acita zabwino zoposa[40].

  • Kristu anatiombola ku temberero la cilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu – Agalatiya 3.13. Anthu ena anena kuti umphawi ndiwo temberero ndiponso kuti ana a Mulungu ataomboledwa ku umphawi adzadalitsidwa ndi cuma. Koma ngati tiwerenga ndime yotsatira m’mutu umenewu tiona kuti Paulo analankhula za dalitso la Mzimu Woyera osati za cuma[41].

  • Pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta – Agalatiya 6.7b. Nthawi zina ndime monga iyi zigwiritsidwa nchito kulimbikitsa anthu kupereka ndalama kwa Mulungu. Ngati tiwerenga ndimeyi ndi mau anzake tiona kuti Mulungu alonjeza madalitso a muyayaya osati a za thupi. Sitikhoza kumpatsa Mulungu ndalama mongofuna kupeza phindu. Sitikhoza kupangitsa Mulungu kutingongola[42].

  • Mukakhala naco cikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kdzakulakani kosacitika – Mateyu 17.20b. Anthu ena anena kuti tifunika cikhulupiriro cabe kucotsa mabvuto (ndiwo monga mapiri) m’miyoyo yathu pakuti tiri nayo mphamvu ya cikhulupiriro. Ngati muwerenga Mateyu 17.14-20 mudzaona kuti Yesu anatanthauza cinthu cina: tiribe mphamvu mwa ife tokha. Ciyambi ca mphamvu yathu si cikhulupiriro cathu, mau athu kapena macitidwe athu, koma tidalira pa Mulungu[43]. Sindife milungu kulamulira mlengamlenga ndi zonse zopezekamo[44].


Tiyenera kuyesa ciphunzitso ciriconse ndi ulaliki uliwonse. Khalani okhazikika!


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya cipunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa; koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira iye amene ali mutu ndiye Kristu – Aefeso 4.14 ndi 15


-------------------------------------------------------------------


[1] 2 Timoteo 4.3, Tito 2.1, [2] Aefeso 5.6, Akolose 2.8, Luka 21.8, [3] 2 Petro 2.1, 1 Yohane 4.1, Macitidwe 17.11, [4] Deuteronomo 4.2, Cibvumbulutso 22.18 ndi 19, [5] Genesis 1 ndi 2, [6] Genesis 3, [7] Yesaya 59.2, Ezekieli 39.24, [8] 1 Yohane 4.10, 2 Akorinto 5.18, [9] Marko 1.15, 1 Yohane 5.1, Ezekieli 36.26 ndi 27, Agalatiya 3.26, [10] Macitidwe 10.43, Macitidwe 26.18, [11] Aroma 8.9, Ezekieli 36.27, [12] Yohane 14.2 ndi 3, [13] Cibvumbulutso 21.27, 1 Akorinto 6.9, [14] 1 Akorinto 14.3, Yona 1.2, [15] Deuteronomo 18.16, Yeremiya 35.15, [16] Mateyu 7.20, Afilipi 2.15, [17] Tito 1.6-8, 1 Timoteo 3.8-13, [18] Yeremiya 28.9, Yeremiya 6.14, [19] 1 Timoteo 4.7, Tito 1.14, 1 Timoteo 1.4, [20] 1 Yohane 4.14, Yohane 1.14, [21] Aefeso 2.1-10, [22] 1 Timoteo 6.10, Marko 10.23-25, Deuteronomo 8.11-15, 1 Timoteo 6.19, [23] Marko 12.41-44 , [24] Luka 16.20-23, [25] Macitidwe 7.59 ndi 60, [26] Ahebri 11.24-26, [27] 2 Akorinto 11.23-28, [28] Zekariya 9.9, Mateyu 8.18, [29] Luka 12.33, [30] Cibvumbulutso 2.18 ndi 19, [31] 2 Timoteo 3.12, Cibvumbulutso 7.14, 1 Petro 5.9, Yohane 15.20, Afilipi 1.29, [32] Ahebri 12.6-10, Aroma 5.3 ndi 4, [33] Mateyu 5.16, 1 Petro 2.12, 2 Atesalonika 1.12, Aroma 12.1, 2 Akorinto 5.15, Akolose 3.23, [34] Yohane 14.6, Ahebri 9.15, Ahebri 4.14-16, Aefeso 2.18, Aefeso 3.12, Mateyu 7.8, [35] Aroma 3.24, Aroma 4.5, [36] Luka 10.7, [37] 2 Akorinto 3.18, Aefeso 2.10, 2 Petro 1.4, 2 Akorinto 4.16 ndi 17, [38] Mika 7.7, Yobu 42.2, Salimo 115.3, [39] Danieli 4.35, [40] Salimo 62.5, Habakuku 2.3, Salimo 119.68, [41] Agalatiya 3.14, Aefeso 1.13, Agalatiya 4.5, [42] Aroma 11.35, 1 Mbiri 29.14, Yobu 41.11, [43] Aefeso 6.10, Afilipi 4.13, [44] 2 Atesalonika 2.3 ndi 4, Deuteronomo 4.39

bottom of page