top of page
Mphatso zazikulu zopatsidwa ndi Mulungu

MPHATSO ZAZIKULU

zopatsidwa ndi Mulungu wamkulu

Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo – Salimo 24.1


Pakuti ngati ambiriwo anafa cifukwa ca kulakwa kwa mmodziyo (Adamu), makamaka ndithu cisomo ca Mulungu, ndi mphatso yaulere zakucokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinacurukira anthu ambiri – Aroma 5.15


Yerekezani kuti muli kuyenda pa mseu. Patapita nthawi muona mwamuna wokalamba wokhala pa mbali ya mseu. Jekete lake lalikulu ndi lobooka-booka. Abvala kabudula wobooka-booka. Aoneka woonda. Ndi codziwika bwino kuti aperewera cakudya mthupi. Mwamuna wobvutika!

Pamene mupitiriza kuyenda, mukomana ndi munthu wogulitsa mathalauza. Mulibe ndalama zambiri, komabe mufuna kugulira mwamunayo wobvutika thalauza. Pobwerera mumpatsa thalauza lake latsopano. Ati kuti akuyamikirani kwambiri cifukwa ca mphatso imene mwampatsa.

M’mawa mukomananso mwamunayo. Thalauza limene munampatsa ndi lobooka-booka kale. Kudziwika bwino kuti mwamuna sanasamalire bwino thalauzi limene adapatsidwa. Mwakhumudwa kwambiri.

Nanga inu mungamve bwanji ngati munthu sasamalira mphatso imene munampatsa?


Ife tonse timalandira mphatso zambiri masiku onse. Izo zapatsidwa ndi Mulungu wamkulu[1]. Kuli Mulungu m’modzi[2]. Tiwerenga za Iye m’Baibulo, Mau ake. Mulungu ndi wamuyaya ndi wokhulupirika, adziwa zonse ndipo ali paliponse[3]. Mulungu ndi Mlengi ndi Mwini wa zonse[4]. Masiku onse tiona cifundo cake, ubwino wake ndi cisomo cake poona zinthu zopatsidwa naye. Tiyeni tiganizireko mphatso zina zopatsidwa ndi Mulungu ndiponso m’mene tiyenera kuyankhako.


Mphatso ya Mulungu: dziko lapansi

Baibulo litiuza kuti Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi[5]. Mulungu sanagwiritse nchito kanthu kalikonse; analankhula ndipo kunacitika[6]. Asanalenge cinthu ciriconse, kunali Mulungu cabe. Mulungu analenga dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Analenga ng’ombe zazikulu ndi udzudzu wamng’ono. Analenga mitengo yaitali ndi maluwa ang’ono. Nsomba, nyerere, zipatso, mbuzi, nyongolotsi, njoka ndi nkhalango; zonse zalengedwa naye. Zonse zolengedwa ndi Mulungu zinali zabwino[7], pakuti Mlengi yemwe ndi wabwino.

Mulungu asamalirabe cilengedwe cake[8]. Ici cichedwa ‘cisamaliro cokonzedweratu ca Mulungu’: alamulira dziko lonse lapansi ndi kulisamalira[9]. M’mawa Mulungu atulukitsa dzuwa kuti tigwire nchito. Alenga njuchi kuti maluwa angatibalire zipatso. Apatsa mvula kuti mbeu zikule. Apangitsa mitengo kuturutsa mpweya wopatsa moyo kuti tipume. Alenga ciswe kupanga zulu kuti tikhale ndi doti yabwino youmbira njerwa. Izi zonse komanso zina ndizo mphatso zopatsidwa ndi Mulungu.

Mulungu ndi Mwini wa dziko lapansi[10]. Anauza munthu kusamalira zonse[11]. Tiyenera kukhala ocenjera kuti sitiononga cilengedwe ca Mulungu. Ganizirani njira m’mene tisamalira nyama, ngakhale tizirombo tating’ono. Tisaononge cilengedwe ca Mulungu mwa kutaya zola za pulastiki ndi zinyalala zina. Ciriconse cimene ticita ciri ndi coturukamo ca cilengedwe ca Mulungu. Tiyenera kusunga bwino cilengedwe mwa kucicitira bwino ndi kupewa zonse zimene zingaciononge.  Mulungu atipatsa cakudya tsiku ndi tsiku[12]; tizimyamikira potipatsa  ndi kusataya cakudya.

Cilengedwe ca Mulungu ndi mphatso yake yapamwamba, ndiye tiyenera kucisamalira ndi mphamvu zathu zonse!


Mphatso za Mulungu: matupi athu

Mulungu analenganso munthu[13]. Anapanga anthu oyamba a pa dziko lapansi: Adamu ndi Hava. Alengabe. Makanda ang’ono asanabadwe alengedwa naye[14]. Matupi athu ndi mphatso zocokera kwa Mulungu.

Matupi athu ndi odabwitsa. Ganizirani maso athu kuona, malilime kulawa, makutu kumva, mapazi kuyenda ndi mau kulankhula. Sitimvetsa m’mene zonse zigwirizana. Mulungu apangitsa matupi athu kugwira nchito. Adziwa zonse za ife[15].

Mulungu ndi Mwini wathu, pakuti anatilenga. Colinga ca kulengedwa kwathu ndi kuti tizilemekeza ndi kupereka ulemu kwa Mulungu[16], ndiye tiyenera kugwiritsa nchito matupi athu kucita tero. Mulungu afuna kuti tisamalira matupi athu mogwiritsa nchito zimene atipatsa komanso mopewa zonse zimene zingawaononge. Ganizirani za kudya kwambiri kapena kusadya zakudya za mitundu yosiyana-siyana. Ganizirani za ukhondo ndi makhalidwe a m’ukwati. Ganizirani za kukhala pa malo abwino ndi opanda zinyalala.

Matupi athu ndiwo mphatso zapamwamba zocokera kwa Mulungu, ndiye tiyenera kuwasamalira ndi mphamvu zathu zonse!


Mphatso ya Mulungu: Baibulo

Mphatso ina imene Mulungu atipatsa ndiyo Baibulo. Baibulo ndi Mau a Mulungu[17]. Ndilo mphatso lapamwamba, cifukwa m’Baibulo, Mulungu adzibvumbulutsa kwa ife[18].

Mulungu ndi wapamwamba ndi wolemekezeka koposa[19]. Iye ndi woyera[20]: wabwino kwambiri ndi wopanda banga. Ife ndife anthu otsutsa Mulungu. Ndife ocimwa: si ndife oyera koma olephera kutumikira Mulungu moyenerera[21]. Ndife odziganizira m’malo mwa kuganizira za kulemekeza Mulungu m’zonse zimene ticita, tikamba ndi kuganiza[22]. Mulungu akuda uchimo[23] ndipo cifukwa cake wocimwa aliyense ayenera kulangidwa ku Gehena muyayaya[24]. Angakhale ndife ocimwa, Mfumu ya mafumu, wamphamvuyonse ndi woyera alankhula nafe m’Baibulo[25]. Ndi codabwitsa!

Mulungu afuna kuti tidziwa kuti sitingakondwere moonadi koma cabe pamene acotsa macimo athu[26]. M’Baibulo Mulungu atiphunzitsa za njira yeniyeni yoomboledweramo ku macimo: mwa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu[27]. Kukhala ndi Baibulo kukaphunziramo ndi koposa kuyetsetsa kwathu ndi ndalama zathu! Baibulo ndilo mphatso yapamwamba yocokera kwa Mulungu, pakuti litiphunzitsa za Yesu Mpulumutsi.


Mphatso ya Mulungu: Yesu Kristu

Kuli mphatso imodzi yofunikira koposa: Yesu Kristu. Mulungu anatuma Mwana wake Yesu kuti Yesu ayanjanitse anthu ocimwa ndi Mulungu[28]. Yesu anafa pa mtanda kumasulira anthu ake ku macimo ao[29]. Iwo abweretsedwa m’ubwenzi wabwino ndi Mulungu, cifukwa ca Yesu Mpulumutsi[30]. Aliyense wolapa ndi kudalira pa Yesu ndi cipulumutso cake ndiye wake[31]. Cipulumutso ca ocimwa mwa Yesu ndico mphatso yapamwamba mwa cisomo[32].

Kodi mwalandira Yesu monga Mphatso yocokera kwa Mulungu kuti akupulumutseni ku mtima wanu wocimwa ndi umoyo wanu wocimwa? Ngati iai, lapani ndi kudalira pa Yesu yekha kuti akupulumutseni. Palibe kalikonse komwe tingacite kuti tingathandize pa kupulumutsidwa kwathu. Kupita ku calichi, kupemphera, kumvera Baibulo ndi kupempha thandizo kwa abusa ndiko kwabwino, koma sikutiyeretsa ku macimo athu[33]. Yesu acita.  Mpempheni zonse zimene mufunika kuti mupulumutsidwe: Yesu afuna kukutumani Mzimu wake Woyera kuti akuphunzitseni[34]. Cifundo ca Mulungu ndi cacikulu!

Ngati Mulungu anakupatsani Yesu ngati Mpulumutsi wanu, myamikireni pa Mphatso yake yapamwamba[35]. Masiku onse Mulungu akusamalirani. Akupatsani zosowa zanu m’umoyo ndi imfa. Khalani umoyo wanu wodzala ndi ciyamiko pa cisomo ndi cisamaliro ca Mulungu. Mlemekezeni m’zonse zimene mucita, pakuti Mulungu ndi wamkulu!


Funani ndi kupeza Mphatso yapamwamba ya Mulungu: Yesu Kristu[36]. Iye ndi woyenera kuposa zonse za pa dziko lapansi.

~

Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwai nu – Mateyu 6.33


[1]Yakobo 1.17, [2] Yesaya 45.5, Yesaya 57.17, [3] Salimo 139.1-4, Mateyu 24.35, Yeremiya 23.24, [4] Aroma 11.36, [5] Genesis 1.1, [6] Salimo 33.6, [7] Genesis 1, Salimo 34.8, [8] Yeremiya 5.24, Macitidwe 14.17, [9] 1 Mbiri 16.31, [10] Salimo 24.1, [11] Genesis 2.15, [12] Genesis 1.29, Mateyu 6.11, Salimo 145.15, [13] Genesis 1.27, [14] Salimo 139.14, [15] Salimo 139, Mateyu 10.30, [16] 1 Akorinto 10.31, Aroma 12.1, 1 Akorinto 6.13b, [17] 2 Timoteo 3.16, Aroma 3.2b, 2 Petro 2.21, [18] Ahebri 1.1, [19] Salimo 91.1, [20] Cibvumbulutso 4.8, [21] Mlaliki 7.20, Yesaya 64.6, Tito 3.3, Aefeso 2.3, Aroma 14.23, [22] Aroma 8.7, [23] Salimo 5.5, [24] Cibvumbulutso 20.15, [25] Yesaya 57.15, [26] Salimo 16.11, Yohane 16.24, Luka 2.10 ndi 11, [27] Yohane 14.6, Macitidwe 10.43, Aefeso 1.7, [28] 1 Yohane 4.10, 1 Petro 2.24, [29] Ahebri 9.28, Ahebri 10.14, 1 Petro 3.18, [30] Agalatiya 4.5, Yohane 1.12, [31] Agalatiya 3.26, Marko 1.15, [32] Aefeso 2.8, [33] Afilipi 3.4-8, [34] Yohane 16.7 ndi 8, Yohane 16.13-15, Tito 3.5-7, [35] 2 Akorinto 9.15, Salimo 34.10, Salimo 48.14, [36] Mateyu 13.45 ndi 46

bottom of page