top of page
IMG-20230614-WA0008_edited.jpg

MINDA
INAI YA M'BAIBULO

Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edene cakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo – Genesis 2.8

 

Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu – Revelation 2.7

 

Minda ndiyo malo kumene kumacitika zambiri. Ndiyo malo kumene anthu amagwira nchito molimba kubzala, kuthirira, kucotsa mbeu zosafunika ndi kukolola. Ku munda anthu amatuluka thukuta, akumva ludzu ndipo alema. Anthu amagwira nchito molimba pakuti afuna mabanja ao kukhala ndi moyo. Komabe nthawi zina anthu adwala pamene ali kugwira nchito ku munda kapena amwalira. Kukhala nthawi ku munda kungabvute kwambiri.

Kukhala ku minda ina ndiko kokondweretsa: anthu akhala pansi kusangalala mthunzi ndi mphepo yabwino. Atenga madzi yozizira m’citsime ndipo akhala ndi mpata yopumula.

M’Baibulo tiwerenganso za minda. M’minda ina munacitika zambiri. Zinthu zacisoni komanso zokondweretsa. Tiyeni tione zimene zinacitika m’minda ya m’Baibulo.

 

Munda wa Edeni

Paciyambi Mulungu analenga zonse[1]. Anauza anthu oyamba, Adamu ndi Hava, kukhala ku munda wokongola womwe Iye adawapangira[2]. Malo awo ndiwo munda wa Edeni[3]. Nthawi zina uchedwa paradaiso.

Munda wa Edeni unali malo wokoma wodzala ndi zipatso zambiri, mthunzi ndi nyama zokoma mtima. Koma kuposa izi zonse kunali mtendere. Mtendere wa Mulungu ndi anthu. Mtendere wa anthu ndi anzao. Mtendere wa anthu ndi cilengedwe cina conse. Zonse zinali zopanda banga[4]. Yerekezani kukhala ku malo abwino otero! Malo kumene mungathyole zipatso  zokoma. Malo kumene mungatenge madzi opatsa mphamvu zatsopano nthawi iriyonse. Malo kumene mungasewere ndi mikango ndi kumene simufunika kuopa njoka. Malo kumene muli pafupi kwambiri ndipo Mulungu. Malo kumene mumakondwera masiku alionse. Ici cingakhala codabwitsa, si mwamene?

Mulungu anauza Adamu ndi Hava kugwira nchito. Anayenera kulamulira dziko ndi zonse zimene zilipo[5]. Mulungu anawaletsa kudya cipatso ca mtengo umodzi woikika[6]. Iwo adzakhala adani a Mulungu ndipo adzamwalira ngati sanamumvere. Mwa kusadya cipatso coletsedwa, Adamu ndi Hava anaonetsa kumvera kwao kwa Mulungu.

Komabe tsiku lina Adamu ndi Hava anadya cipatso ca mtengo woletsedwa[7]. Anacimwa. Zonse zinasinthika mwamsanga. Ndipo zinasinthikatu! M’malo mwa kusangalala ciyanjano ca Mulungu, Adamu ndi Hava anamubisalira[8]. M’malo mwa kukondwera pokhala pamodzi m’cikondi, mtendere ndi mgwirizano, iwo anayamba kuikirana mlandu[9]. M’malo mwa kusangalala cilengedwe ca Mulungu, iwo anakomana ndi mabvuto ambiri[10]. Cinaipa kwambiri!

Zotsatira za kusamvera kwao zikhuzanso ife ndi miyoyo yathu. Baibulo likamba kuti ndife ana a mkwiyo cibadwire[11]. Citanthauza kuti Mulungu akalipa ndi ife cifukwa ca macimo athu. Mkwiyo wa Mulungu ndiwo cinthu cimene tiyenera kuopa!

Cotsatira cina ca chimo loyamba ndi cakuti tiyenera kuthana ndi mabvuto pakati pa ife ndi anthu ena. Tiyenera kuthana ndi kudzikonda, kudana, nsanje, kudzikweza, kusakhulupirira ndi zina zotere. Macimo awa acokera m’mitima yathu yocimwa[12]. Baibulo likamba kuti munthu wina aliyense ali ndi mtima wocimwa[13].

Kuposa izi zonse tiyenera kuthana ndi matenda, imfa ndi zoopsa. Tingatenthedwe ndi moto, tingamire m’madzi ndipo tingalumidwe kapena kuphedwa ndi nyama. Imfa ndiyo cotsatira ca imfa[14].

Munda wa Edeni utiphunzitsa kuti ife tonse talekanitsidwa ndi Mulungu cifukwa ca macimo.

 

Munda wa Getsemane

Mulungu sanakondwere ndi msintho uwo waukulu ndi woipa kwambiri. Komabe Iye anapanga njira kuyeretsa anthu ku macimo ao[15].  Mwa kukhululukira macimo ao, Mulungu angakonzenso zonse zimene zaonongeka[16]. Mwamsanga atangocimwa Adamu ndi Hava, Mulungu analonjeza kutuma Wina kugonjetsa zoipa zonse[17]. Winayo ndi Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.

Yesu anatsika Kumwamba nabadwa pa dziko lapansi[18]. Timakumbukira kubadwa kwake pa tsiku la Krisimasi. Anakhala moyo wake momvera Mulungu. Sanacimwe konse[19]. Koma Satana sanafune Yesu kukhala Mpulumutsi: anafuna anthu kulekanitsidwa ndi Mulungu nthawi zonse. Ndipo anthunso sanafune Yesu kukhala Mpulumutsi: anaganiza kuti angafike Kumwamba mwa mphamvu yao mwa kuyesa kusunga malamulo a Mulungu. Anamzonda ndi kuzunza Yesu[20].

Mulungu analola Yesu Mwana wake kuzunzidwa pakuti njira iyo inali njira yeniyeni yakuti Yesu anakhoza kukhala Mpulumutsi[21]. Ndipo Yesu anabvomera kuzunzidwa pakuti anafuna kukhala Mpulumutsi wa anthu ocimwa[22].

Yesu anakanidwa ndi kunyozedwa umoyo wake wonse koma ku mapeto a moyo wake kuzunzika kwake kunali koipa koposa. Kunalinso koipa kuposa m’mene munthu wina aliyense anazunzika pakuti Yesu ananyamula macimo onse[23].

Usiku wina Yesu anali m’munda wa Getsemane[24]. Kumeneko Yesu anali m’ziphinjo zazikuli ndi ululu. Anabvutika cifukwa ca macimo. Osati cifukwa ca macimo a Iye mwini, koma cifukwa ca macimo a anthu ake! Anatenga zolakwa zonse, macimo onse ndi zoipa zonse[25]. Kuzunzika kwa Yesu kunali kwakululu kotero kuti thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi[26]. Atazunzidwa Yesu m’munda wa Getsemane, Iye anatengedwa kapolo, anafunsidwa mafunso ndi atsogoleri, anacitidwa nkhanza, ananyozedwa ndi kukhomedwa pa mtanda[27]. Anamwalira[28].

Munda wa Getsemane utiphunzitsa za mkwiyo wa Mulungu cifukwa ca macimo.

 

Munda wa Yosefe wa Arimateya

Yosefe wa Arimateya poona kuti Yesu adamwalira, anapempha cilolezo kucotsa mtembo wa Yesu ku mtanda ndi kuuika mtembowo m’manda[29]. Anaika mtembo wa Yesu m’munda wa iye mwini wochedwa munda wa Yosefe wa Arimateya. Patapita masiku atatu azimai ena obwera kuika thupi la Yesu mankhwala  anali odabwa popeza manda wa Yesu wotseguka. Anakomana ndi mngelo amene anawauza kuti Yesu adauka kwa akufa[30]. Yesu anasonyeza kuti sanagonjetse cabe macimo mwa imfa yake pa mtanda komanso kuti mwa kuuka kwake anagonjetsa cotsatira ca macimo ndico imfa[31]!

Ici ndi codabwitsa. Yesu ali ndi moyo ndipo apatsa umoyo wa uzimu kwa iwo akufa m’uzimu cibadwire[32]. Ndico cisomo cacikulu!

Munda wa Yosefe wa Arimateya utiphunzitsa kuika ciyembekezo cathu kwa Yesu Kristu amene anagonjetsa macimo ndi imfa.

 

Munda womuyaya: Paradaiso

Cifukwa ca zimene Yesu anacita, ife anthu ocimwa tikhoza kukhululukidwa ku macimo athu[33]. Tiyenera kudalira pa Yesu yekha. Ici citanthauza kulapa: kumva cisoni pa zolakwa zathu, kuleka kucita zoipa ndi kupempha Mulungu cikhululukiro mwa Yesu. Citanthauzanso kukhulupirira Yesu: kudzipereka kwa Iye. Sicitanthauza kudalira pa cinthu ciriconse ca ife mwini. Kupita ku calichi sikutiyenera kupulumutsidwa. Ngakhale kupereka cakhumi, kukhala ndi makhalidwe abwino, kubatizidwa kapena cinthu cina sitiyenera kuti tipulumutsidwe. Kulibe ciriconse cimene cithandiza kuti tipulumutsidwe koma Yesu afuna kulandira wina aliyense amene adza kwa Iye[34].

Aliyense amene alandira Yesu kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi mwa cisomo, ayanjanitsidwa ndi Mulungu[35]. Mulungu awasamalira masiku onse a miyoyo yao. Ndiwo anthu a Mulungu ndi ana ake. Adzaloledwa kukhala naye Kumwamba imene ichedwanso Paradaiso[36]. Ndiyo malo kumene kulibe kuzunzidwa, misozi, njala ndi mdima[37]. Ndi malo a abwino kuposa zimene tingayerekeze.

Pandunji pa Paradaiso kapena Kamwamba ndi Gehena. Gehena ndi malo oipa kuposa tingayerekezeko. Ndiwo malo kumene Satana akhalako pamodzi ndi iwo onse amene amumvera m’malo mwa kumvera Mulungu[38]. Ndiwo malo kumene anthu anyamula cipsinjo cosazolowereka ca macimo ao. 

Koma Yesu akhalabe okonzeka ndi ofuna kukhululukira macimo anu kotero kuti inunso mudzakhala naye ku Paradaiso muyayaya. Lapani macimo anu ndipo khulupirirani Yesu Mpulumutsi!

----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

[1] Genesis 1 ndi 2, [2] Genesis 2.15, [3] Genesis 2.8 ndi 9, [4] Genesis 1.31, [5] Genesis 2.15, [6] Genesis 2.16-17, [7] Genesis 3.6, [8] Genesis 3.8, [9] Genesis 3.12, [10] Genesis 3.13-20, [11] Aefeso 2.13, [12] Marko 7.21-22, [13] Yobu 15.14, Mlaliki 7.20, Miyambi 20.9[14] Aroma 6.23, Aroma 5.12[15] Yeremiya 33.8-9, Ezekieli 36.33, Tito 2.14, [16] Cibvumbulutso 21.1, 2 Akorinto 4.16, Acts 3.21, 2 Akorinto 5.17, [17] Genesis 3.15, [18] Luka 1.26-35, Luka 2.6-7, Aefeso 4.10, [19] 2 Akorinto 5.21, 1 Yohane 3.5, [20] Yohane 15.25, [21] 1 Yohane 2.2, Luka 22.22, 1 Yohane 4.10, [22] Aefeso 5.2, Ahebri 10.5-7, [23] 1 Yohane 2.2, 1 Yohane 4.14, [24] Mateyu 26.36-46, [25] Yesaya 53.6, 1 Petro 3.18, [26] Luka 22.44, [27] Mateyu 26 ndi 27, [28] Marko 15.37, [29] Mateyu 27.57-60, [30] Mateyu 28.1-6, [31] 1 Akorinto 15.54-57, [32] Aefeso 2.1-6, [33] Macitidwe 2.38, 1 Akorinto 5.21, Agalatiya 2.16, 1 Yohane 4.9, [34] Yohane 6.37, [35] Akolose 1.21, Aroma 5.10, [36] Cibvumbulutso 2.7, [37] Cibvumbulutso 21.4, [38] Mateyu 25.41

bottom of page