CUMA CA M'BAIBULO
Home
Nkhani za m'Baibulo
Mavidiyo
Nyimbo
Maphunziro ena
Za ife
More
Ambuye Yesu anapulumutsa mwamuna ku macimo ake
namciritsa. Yesu ali ndi mphamvu zonse. Akwaniritsa kutipulumutsa. Pemphani Ambuye!
Yesu anauza fanizo la Mfarisi ndi wamsonkho. Wamsonkho anapempha Mulungu cikhululukiro. Tizipemphanso cikhululukiro ca macimo athu, cifukwa Mulungu amamva mapemphero otere.
Yesu anabadwa pa dziko lapansi.Abusa anabwera kumlemekeza. Pamene Yesu abadwa m'mitima yathu, ndife opulumutsidwa ku macimo athu.
Yesu anauza fanizo la mbusa wabwino. Yesu ndiye Mbusa Wabwino!
Yesu anauza fanizo la mwana wa mwamuna wolowerera. Mulungu afuna ife kubwerera kwa Iye!
Yesu anatsegula maso a Bartimeyu wakhungu.
Yesu angatsegule mitima yathu yakhungu.
Yesu anauza fanizo la anamwali.
Ife tiyenera kuitana kwa Ambuye tsopano, nthawi ikalibe kutha.
Yesu anauza fanizo kutiphunzitsa kuti tiyenera kukonda ndi kuthandiza wina aliyense.
Yesu anauza fanizo kutiphunzitsa za cuma ceniceni.
Yesu anauza fanizo kutiphunzitsa kuti anthu amene akhulupiriradi mwa Iye adzapulumutsidwa mulimonse m'mene zingakhalire.
Filipo anaphunzitsa mdindo za Yesu. Mdindo anatembenuka kupyolera mwa Mzimu Woyera ndi Mau a Mulungu. Tiyenera kumvera mwaulemu ku Mau a Mulungu ndi kumpempha Mulungu kuti atitembenuza.