Malamulo a Mulungu; malangizo athu
Cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi nchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo – Aroma 3.20
Momwemo cilamulo cidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro – Agalatiya 3.24
Pa mbali pa mseu waukulu pali zikwangwani zimene zitionetsa njira ku mizinda, midzi ndi masitolo. Ngati sitiziona, tingasowe njira mosacedwa.
Baibulo litionetsanso njira imene tiyenera kupitako m’moyo wathu. Mulungu atipatsa malamulo ake kutiphunzitsa zimene akhumba kwa anthu ake kuti iwo akhale oyenera[1]. M’Eksodo 20 tipeza malamulo odziwika ngati Malamulo Khumi[2]. Tiwayang’anire ndi kuwerengetsa umoyo wathu!
1. Mulungu m’modzi – Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha[3]
Kuli Mulungu m’modzi[4]. Analenga zonse[5]. Iye yekha alamulira[6]. Cifukwa cace afuna kuti tizimumvera ndi kusiya konse mafano, ufiti, zikhulupiriro zacabe komanso cikhulupiriro ca mu oyera mtima, mizimu ndi anthu[7]. Tizithokoza, tizikonda ndi kumlemekeza Mulungu ndi mtima wathu wonse kotero kuti tidzipereka kwa Iye modzicepetsa[8].
2. Kufanizira Mulungu – Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse (…); usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje (…)[9]
Mulungu ndi Mzimu woyera ndi woyenerera[10]. Cifaniziro ciriconse tingapange kumfanizira Mulungu ndico coperewera ndi comnyogodola[11]. Mulungu safuna kuti timlemekeza kudzera mwa zithunzi, mizimu kapena anthu[12]. Afuna kuti tizimdziwa ndi kumpembedza monga atilamulira m’Mau ake, Baibulo[13].
3. Dzina la Mulungu – Usachule dzina la Yehova Mulungu wako pacabe (…)[14]
Dzina la Mulungu litiuza m’mene Mulungu aliri[15]. Pamene tichula dzina lace pacabe, timnyoza. Timnyozanso ngati tichula dzina lace mobwezerabwezera, mosaganizira ndi mosasamala pa nthawi yopemphera. Ticitira cipongwe Mulungu pamene tinena dzina lake potemberera, ponyenga kapena polumbira lumbiro losafunika[16]. M’malo mwa izi, tizichula dzina la Mulungu mwa mantha ndi ulemu pakuti Mulungu ndi wamkulu kwambir[17]i! M’zonse zimene tinena, tiganiza ndi kucita, tizilemekeza Mulungu ndi kuthandiza anthu ena kucita cimodzimodzi[18].
4. Tsiku la Mulungu – Uzikumbukila tsiku la Sabata, likhale lopatulika (…)[19]
Mulungu afuna kuti tiziganizira Iye yekha pa tsiku la Sabata[20]. Kucokera pa nthawi ya Cipangano Catsopano, tsiku la Ambuye ndi pa Sondo[21]. Pa tsiku lake timapita ku calichi kumvera Mau ake m’Baibulo, kumtamandira, kupemphera ndiponso tipeza njira zocitira cifundo anthu obvutika[22]. Tsiku la Sondo licititsa cidwi ca Akristu obadwa mwatsopano za Kumwamba. Cifukwa ca Mpulumutsi wao, iwo adzakhala Kumwamba kuti akhale oganizira Mulungu yekha ndi kupeza cisangalalo m’kupezeka kwake[23]. Coyembekezera ici ciwalimbikitsa kufunafuna kupezeka kwa Mulungu masiku onse ndiponso kudziletsa zoipa zonse[24].
5. Maulamuliro athu – Uzilemekeza atate wako ndi amako (…)[25]
Mulungu atipatsa anthu amene ali ndi ulamuliro kuli ife, mwacitsanzo makolo, aziphunzitsi, mafumu ndi pulezidenti. Tiyenera kuwaonetsa ulemu, cikondi ndi kukhulupirika mwa kuwamvera[26] (osati ngati afuna kuti ticitira mwano Mulungu[27]).
6. Kuteteza umoyo – Usaphe[28]
Mulungu atiletsa kucita ciriconse cimene ciononga munthu aliyense m’njira iriyonse. Sitiloledwa kunyazitsa, kuda, kukhala wansanje, kupweteka kapena kupha munthu mwa maganizo, macitidwe ndi mau ngakhale kulankhula ndi manja kapena maso cabe[29]. Koma tizikonda mnzathu monga tidzikonda ife mwini ndiponso kuwaonetsa cikondi ndi cifundo[30]. Tiyenera kuteteza mnzathu (ngakhale adani athu) ndiponso ife mwini pa zonse zimene zingaononge thupi lathu kapena mzimu wathu[31].
7. Ciyeretso – Usacite cigololo[32]
Mulungu ndi woyera ndipo akuda cidetso conse. Tizikhala mosadzidetsa m’banja komansa kunja kwake[33]. Matupi ndi mizimu ya Akristu obadwa mwatsopano ndizo za Mulungu woyera[34], ndiye tiyenera kuzisunga zopanda cidetso mwa kuthawira konse zodetsa zonse za m’macitidwe, mau, malingaliro ndi makumbo[35].
8. Zinthu zathu – Usabe[36]
Mulungu akuda njira zonse za kuba, kunyenga ndi kukhala wadyera[37]. Afuna kuti tizikhala okhutira ndi zonse zimene atipatsa mwa nchito zathu komanso kuti tizisamalira bwino kuti tikhala osaumira[38].
9. Umboni wathu – Usamnamizire mnzako[39]
Mulungu akonda coonadi. Satilola kunama wotsutsa munthu aliyense, kupotoza mau a munthu wina ndiponso kucita thonjo kapena kusinjirira[40]. Sitiziweruza kapena kubvomereza poweruza aliyense mothamanga kapena mopanda kumvetsetsa[41]. Tizipewa bodza lirilonse koma kukonda coonadi[42].
10. Zilakolako zathu – Usasirire (…) kanthu kali konse ka mnzako[43]
Zilakolako zocimwa zoturuka m’mtima wathu ndizo ciyambi ca macimo ena onse[44]. Cifukwa cake Mulungu satilola kufuna kali konse ka mnzathu[45]. Koma tiyenera kukondwera m’cilungamo conse[46]: ici citanthauza kusirira zabwino ndi kusunga malamulo onse moonadi ndi mtima wonse[47].
Yesu anakwaniritsa malamulo a Mulungu
Poona Malamulo Khumi, tiyenera kubvomereza kuti ndife ocimwa: taphwanya malamulo onse a Mulungu. Kulibe munthu woyenera momwe Wopanga malamulo afuna[48].
Cifukwa ca macimo athu, tiyenera kukhala kutali kwa Mulungu m’umoyo ndi kukhala ku Gehena titamwalira[49]. Kulibe ciyembekezo ciriconse kuti tingafike Kumwamba mosunga malamulo a Mulungu[50]. Ngakhale zocita zathu zabwino sizingatipulumutse, komabe udindo wathu ndi kumvera Mulungu. Tiyenera kumvetsa ndi kubvomereza kuti tifunika Wina kutipulumutsa ku macimo athu ndi kutiyeretsa pa maso pa Mulungu. Winayo ndi Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu[51].
Yesu Kristu anacita zonse zimene sitingakwaniritse konse[52]!
Pa tsiku la Krisimasi tikumbukira kuti Yesu anadza kukhala pa dziko lapansi momvera Mulungu[53]. Anasunga konse malamulo a Mulungu[54].
Pa tsiku la Licanu Loyera tikumbukira kuti Yesu anafa pa mtanda kukhala ciombolo m’malo mwa onse odalira pa cipulumutso cake[55].
Pa tsiku la Paska tikumbukira kuti Yesu anauka kwa akufa: anagonjetsa imfa, ndiyo mphotho ya uchimo[56].
Pa tsiku lokumbukira kukwera Kumwamba tikumbukira kuti Yesu anabwerera Kumwamba ndiponso kuti Iye ndi Mfumu ya anthu ake onse amene afuna kumlondola momvera[57].
Pa tsiku la Pentekoste tikumbukira kuti Yesu anatuma Mzimu wake Woyera kuphunzitsa anthu ocimwa kulapa ku macimo ao ndi kudalira pa Yesu popeza cipulumutso[58].
Tsiku lina Yesu adzabweranso ndi kutenga anthu ake naye[59]. Osati cifukwa iwo anakhala ndi moyo woyenerera, koma cifukwa Iye anawapatsa mwa cisomo umoyo wake wosacimwa[60]. Kumwamba iwo adzakhala naye muyayaya ndi kumlemekeza momvera kwambiri[61].
Thawirani kwa Yesu kupulumutsidwa ku macimo anu, khalani wochangu kucita nchito zabwino, mosaleka kupempha Mulungu kuti akukonzanso mwatsopano ku cifanizo cake kuti muzimumvera ndi kumlemekeza[62].
~
Pakuti Kristu ali cimariziro ca lamulo kulinga ku cilungamo kwa amene ali yense akhulupira – Aroma 10.4
---------------------------------------------------
[1] Miyambi 19.16, Mateyu 5.48 [2] Eksodo 20.1-17 [3] Eksodo 20.3 [4] 1 Samueli 2.2, Deuteronomo 4.35 [5] Genesis 1 ndi 2 [6] Yeremiya 10.7 [7] 1 Yohane 5.21, Deuteronomo 8.9-12, Mateyu 4.10 [8] Mateyu 22.37, Salimo 111.10, 1 Petro 5.6 [9] Eksodo 20.4-6 [10] Yesaya 6.3, Yohane 4.24 [11] Yesaya 40.18, Aroma 1.23 ndi 24 [12] Numeri 33.52, 2 Mafumu 18.4 ndi 5 [13] 1 Samueli 15.22 ndi 23 [14] Eksodo 20.7 [15] Eksodo 3.14 [16] Levitiko 24.10-14, Levitiko 19.12, Yakobo 5.12 [17] Salimo 99.1-5, Levitiko 5.1 [18] Akolose 3.17 [19] Eksodo 20.8-11 [20] Eksodo 31.13-17, Levitiko 23.3 [21] Macitidwe 20.7, Aroma 10.14-17 [22] Salimo 68.26, Ahebri 10.23-25, 1 Timoteo 2.1, Akolose 3.16 [23] Yohane 14.3, Ahebri 4.9-11, Cibvumbulutso 21.11 [24] Miyambi 8.13, Aroma 12.9 [25] Eksodo 20.12 [26] Aroma 13.1 ndi 2, Mateyu 22.21, Miyambi 23.22, Aroma 13.1-8, Akolose 3.18-21, 1 Petro 2.18 [27] Macitidwe 5.29 [28] Eksodo 20.13 [29] Genesis 9.6, Mateyu 26.52, Aroma 1.29, Miyambi 14.30, Aroma 12.19, 1 Yohane 2.9-11, 1 Yohane 3.15 [30] 1 Petro 3.8-12 [31] Mateyu 5.44 ndi 45, Aroma 12.20 [32] Eksodo 20.14 [33] Aefeso 5.3-5, 1 Atesalonika 4.3-8 [34] 1 Akorinto 6.19 [35] Mateyu 5.27-30, 1 Akorinto 15.33 [36] Eksodo 20.15 [37] Deuteronomo 25.13-16, Luka 16.13, Luka 6.35, Luka 12.15, Yakobo 5.1-6 [38] Miyambi 21.20, Ahebri 13.5, Aefeso 4.28 [39] Eksodo 20.16 [40] Miyambi 19.5, Miyambi 12.22, Levitiko 19.12 [41] Mateyu 7.1, Miyambi 13.5 [42] 1 Akorinto 13.6, Aefeso 4.25 [43] Eksodo 20.17 [44] Marko 7.23 [45] Miyambi 3.24, 1 Timoteo 6.9 ndi 10 [46] 1 Timoteo 6.6 [47] Yesaya 33.15 [48] Aroma 3.23, Yakobo 2.10, 1 Yohane 1.8, Mlaliki 7.20 [49] Miyambi 15.29, Salimo 5.4, Mateyu 25.45 ndi 46, Nahumu 1.2 [50] Agalatiya 3.10, Aroma 3.20, Agalatiya 2.16 [51] Mateyu 1.21, 1 Timoteo 2.5, 1 Akorinto 1.30 [52] 2 Akorinto 5.21 [53] Luka 2, Afilipi 2.8 [54] Mateyu 5.17 [55] Luka 23, Marko 10.45, Yohane 3.16 ndi 36 [56] Mateyu 28, Aroma 6.23, 1 Akorinto 15.55 [57] Macitidwe 1.6-11, Marko 16.19, Yesaya 33.22, Yohane 14.15 [58] Macitidwe 2, Macitidwe 2.38 [59] Yohane 14.3 [60] Aefeso 2.9, Aroma 3.21-25, Aroma 5.16 [61] Cibvumbulutso 7.15 [62] Yesaya 45.22, Yohane 6.40, Aefeso 2.10, Aroma 8.29, 2 Akorinto 3.18