top of page
Ndipo macimo athu atineneza ife - Yesaya 59.12
Ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse - 1 Yohane 1.7
Ndife ocimwa
Tili ndi macimo ambiri[1]. Baibulo ikamba kuti anthu onse ndi ocimwa[2].
Mulungu amaona mu mitima ndiye amadziwa zonse zimene zili mu mitima yathu[3]: zimene tiganiza, tinena ndi kucita.
Ganizirani za umoyo wanu: munacita zambiri zimene Mulungu safuna ndipo simunacite zimene Mulungu alamula[4]. Ganizirani za mtima wanu: ngakhale cikhalidwe canu cinali cabwino, mu mtima mwanu munali macimo monga nsanje, udani ndi kunena mabodza. Cifukwa ca macimo awa ndife ocimwa.
Ndife ocimwa, ofooka ndi oipa. Ndi cofunikira kwambiri kuti tiulule macimo athu. Sitingathe kukhala olungama popanda kudziwa kuti ndife ocimwa.
Funsani Mulungu kuti Iye akuonetseni macimo anu cifukwa ndi Iye Yekha amene angakuzindikiritseni macimo anu.
Macimo athu ayenera kucotsedwa
Mulungu ndiye woyera ndipo Iye amadziwa zonse[5]. Pamene tizamwalira azatiweruza. Iye amadziwa macimo athu. Muzindikire kuti kukhululukidwa ku macimo anu ndi kofunikira kuti mukaloledwe m’mwamba ndi kukhala ndi Yesu. Ngati macimo anu sazakhululukidwa muzakhala kuGehenna.
Anthu ena amaganizira kuti zinthu zofunikira ndi cakudya, zobvala, ndalama, banja ndi kukhala osangalala. Ena amaganizira kuti kupita kuchalici kapena kusamalira odwala ndico coposa. Koma m’cikhulupiriro ca Khristu tiyenera kudziwa ndi kukhulupirira kuti macimo athu anakhululukidwa. Mulungu anena m’Mau ake kuti muyenera kufunafuna Ufumu wa Mulungu ndi cilungamo cace koposa zonse[6].
Sitikhoza kudziyeretsa
Sitikhoza kuziyeretsa ife tokha, cifukwa:
Kutembenuka ndi kumva cisoni kwa zoipa zathu sikukhoza kuticotsera macimo athu
Kucita zimene Mulungu amafuna (monga kupita kuchalici ndi kuwerenga Baibulo) sikutipatsa kukhululukidwa kwa macimo[7]
Anthu ena samakhoza kutiyeretsa ku macimo athu[8]
Kulibe cinthu ciliconse cimene cingatipatse mtendere ndi Mulungu. Kulibe munthu aliyense amene angatipatse mtendere ndi Mulungu.
Kuyeretsedwa ndi mwazi wa Yesu
Mwazi wa Yesu wokha ungatiyeretse. Mwazi wa Yesu ndi mwazi umene Yesu anakhetsa pamene Iye anamwalira pa mtanda cifukwa ca ocimwa.
Mulungu analonjeza mwazi wa Yesu[9]. Iye ananena kuti kuzakhala Munthu amene azagonjetsa Satana.
Mwazi wa Yesu ndi wamtengo wapatali wa Mulungu cifukwa Yesu ndi Mulungu. Yesu anamwalira m’malo mwa ocimwa. Cifukwa ca mwazi wa Yesu, Mulungu ndi anthu ocimwa angakhale pamodzi. Pa kumwalira pa mtanda Yesu analipirira zolakwa za ocimwa.
Mwazi wa Yesu ungatiyeretse, ngakhale tinacita macimo ambiri[10]. Kulibe cimo limene silingakhululukidwe ndi Yesu.
MUNGAYERETSEDWE KU MACIMO ANU ONSE!
Cifukwa ca mwazi wa Yesu, ana a Mulungu ali ndi mtendere ndi ciyembekezo mwa Mulungu. Ndi olungama pa maso pa Mulungu cifukwa ca mwazi wa Yesu. Mwazi wa Yesu uli ndi mphamvu zopambana macimo onse.
Cikhulupiriro ndi cofunikira
Cikhulupiriro ndi cofunikira kwambiri kuti mwazi wa Yesu ukuyeretseni[11].
Kupita kuchalici, kudya Mgonero wa Ambuye, kapena kukhala obatizidwa sikungakuyeretseni ku macimo anu.
Ndi cikhulupiriro cokha cimene cingakupatseni zinthu zabwino zimene Yesu anapeza pa mtanda pamene anafa. Kukhulupirira sikutanthauza kudziwa zimene zili m’Baibulo cabe komanso kumva cisoni cifukwa ca macimo anu ndi kukhulupirira kuti Yesu analipirira macimo anu.
Simukhoza kupatsa Mulungu cinthu ciliconse kuti Iye akakhululukireni macimo anu koma mwazi wa Yesu ungakuyeretseni. Uthenga wabwino ndi wakuti Mulungu angakupatseni zilizonse zimene mufunikira kuti mupulumutsidwe[12]. Ndi Mulungu Mzimu Woyera Yekha amene akhoza kukupatsani ici mwa cisomo. Cifukwa ca ici muyenera kupemphera Iye kuti akupatseni cikhulupiriro kuti macimo anu akhululukidwe.
Funso
Muyenera kudziwa za macimo anu. Sindifunsa mumapita kuchalici kuti kapena mumamvera abusa oti. Sindifunsa zimene mufuna kucita mu umoyo wanu koma ndikufunsani: ‘Kodi macimo anu ali kuti?’
Kuli malo awiri cabe kumene macimo anu angakhale.
Macimo anu amakhala pa inu nokha; osakhululukidwa ndi osayeretsedwa.
Macimo anu angakhale pa Khristu; okhululukidwa ndi oyeretsedwa.
Ganizirani pa izi. Muziyese inu nokha. Muyankhe funso ili: ‘Kodi macimo anga amakhala pa ine kapena pa Yesu?’
Kuitanidwa
Ngati macimo anu sanakhululukidwe: pitani kwa Yesu mwa pemphero kuti mukhululukidwe macimo anu. Ndi kotheka kuti muli ndi macimo ambiri kapena simunakhulupirire pamene munali ang’ono. Ndi kotheka kuti anthu kapena Satana amanena kuti muli oipa koposa kuti simungakhululukidwe. Ndi kotheka kuti Satana amafuna mudzimulemekeza. Mudziwe ici: Yesu akhoza kupulumutsa onse amene akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye[13].
Mulungu sasintha. Pitani kwa Iye ndipo mwazi wake uzakuciritsani ku macimo anu onse.
Ngati simudziwa cocita: uzani Yesu! Uzani Yesu kuti muli ndi macimo ambiri, muuzeni zonse zimene muganiza ndipo pemphani Iye kuti akukhululukireni.
Cilimbikitso
Kwa iwo amene anaphunzitsidwa ndi Mzimu Woyera za macimo ao ndipo anathamangira kwa Yesu: “Gwiririrani Yesu”. Munali ocimwa pamene munathamangira kwa Yesu ndipo mumacitabe macimo.
Gwiririrani Yesu ndipo funsani cikhululukiro ca macimo amene mwakhala muli kucita.
Gwiririrani Yesu ndipo onetsani dziko lapansi kuti mumkonda Yesu. Citani zimene Mulungu alamulira[14]. Khalani oyera ndi okondana ndi anthu ena.
Gwiririrani Yesu ndipo lemekezani Yesu cifukwa ca zimene anacita kukupululumutsani.
Gwiririrani Yesu ndipo ganizani nthawi zonse kuti macimo anu anakhululukidwa mwa mwazi wa Yesu Yekha.
Ndipo mundiyeretse kundicotsera coipa canga - Masalmo 51.2
---------------
[1] Yakobo 3.2 [2] Aroma 3.10, Aroma 5.12, 1 Yohane 1.8 [3] 1 Samueli 6.7 [4] Eksodo 20.1-17, Mateyu 25.41-46 [5] Habakuku 1.13 [6] Mateyu 6.33, Salimo 32.1 ndi 2 [7] Aroma 3.20 [8] Salimo 49.7 [9] Genesis 3.15 [10] Yeremiya 1.18 [11] Aroma 3.25, Yohane 3.36, Macitidwe a Atumwi 13.39, Aroma 5.1 [12] Aefeso 2.8 [13] Ahebri 7.25 [14] Mateyu 22.37-40
bottom of page