Cisamaliro ca Mulungu m'kati mwa mabvuto
M’dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine – Yohane 16.33b
Ndipo tithamange mwacipiriro makaniwa adatiikira, ndi kupenyera woyambira ndi womariza wa cikhulupiriro cathu, Yesu – Ahebri 12.1 ndi 2
Kodi munaonako ana ang’ono kucita mantha? Kapena ana ang’ono kupweteka pamene aterereka ndi kugwa? Pamene ana akumva cisoni, iwo apfuula kupempha thandizo. Afunika makolo ao kuwatonthoza kapena kuthetsa mabvuto ao. Makolo angacite zatheka koma sakwaniritsa kucitira ana ao zonse zimene afuna nthawi zonse. Kuli M’modzi amene salephera. Wosamalirayo ndi Wopatsayo ndiye Mulungu.
Wosamalira wabwino
Kale kwambiri kunalibe cinthu ciriconse koma Mulungu cabe[1]. Pa nthawi iyo Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi: analankhula ndipo kunacitika[2]. Mulungu anazilenga pakuti anafuna tero. Zonse zimene Mulungu afuna ndi zabwino[3]. Kulibe wina wopambana Iye amene angauze Mulungu kucita ciani[4]. Iye yekha ndiye wolamulira. Analenga madzi, mitengo, maluwa, tizirombo, zipatso ndi zina zonse zimene tiona mbali zonse za dziko lapansi. Mulungu analenganso Adamu ndi Hava[5]. Iwo anali anthu oyamba pa dziko lapansi. Zonse zimene Mulungu analenga zinakhala zabwino kwambiri ndi zopanda banga[6]. Mulungu anakonda zonse zimene Iye adalenga. Adamu ndi Hava anazikondanso. Kopambana zonse iwo anakonda Mulungu. Iye anawasamalira[7]. Masiku onse Mulungu analankhula nao[8]. Iwo anakhala m’mgwirizano ndi Mulungu. Adamu ndi Hava ankamvera Mulungu. Ici cinali monga Mulungu anawayembekezera kucita[9]. Adamu ndi Hava sanasowe cinthu ciriconse.
Wosamalira wamphamvu
Mulungu amasamalira zonse mwa mphamvu[10]. Kulibe ciriconse cimene cingamleketse kucita zimene Iye afuna[11]. Mulungu sangalepheretsedwe ndi munthu, mzimu kapena cocitika[12]. Kulibe ciriconse cimene siciri m’ulamuliro wake, ngakhale m’miyoyo yathu. Nthawi zina zingaoneke monga tilamulidwa ndi umwayi. Tingaganize kuti zinthu zina m’miyoyo yathu sizilamuliridwa ndi Mulungu. Koma Baibulo likamba kuti Mulungu acita zonse monga mwa uphungu wa cifuniro cace[13].
Wosamalira wacifundo
Ngakhale Adamu ndi Hava anakhala okondwa, iwo anasankha kusamvera. Anadya cipatso ca mtengo womwe Mulungu anawaletsa kudya[14]. Zonse zinasinthidwa cifukwa ca kusamvera kwao[15]. Tsono tikomana ndi zinthu zambiri zoipa m’umoyo, monga matenda, imfa, kusagwirizana, umphawi ndi kugwiritsa zinthu mosayenera. Mitima yathu inasandukanso yoipa[16]: itipangitsa kucita, kuganiza ndi kunena zoipa, monga kudzikweza, nsanje, umbombo, kusakhulupirira, kudzikonda ndi msulizo. Tsono tifuna Mulungu kutitumikira, m’malo mwa ife kutumikira Mulungu[17]. Zinthu izi ndi zina zambiri zichedwa macimo. Anthu onse acita macimo ambiri[18]. Cifukwa ca mitima yathu yocimwa, ndife olekanidwa ndi Mulungu ndipo tiyenera kukhala m’Gehena muyayaya, kutali kwa Mulungu[19]. Palibe njira kuti tingadzipulumutse ku macimo athu[20].
Kodi Mulungu analeka kusamalira cilengedwe cace cifukwa ca macimo athu? Iai, sanaleke[21]! Amasamalirabe dziko lapansi ngakhale masiku ano. Atisamalirabe. Atipatsa zofunikira zathu: mvula, cakudya, dzuwa, malo okhalapo ndi zina zambiri. Tidalira konse pa Iye kuti tikhalabe ndi moyo. Mwa cisomo Mulungu amasamalira anthu amene amcimwira[22].
Tiona cifundo ceniceni ca Mulungu pamene tiyang’ana Yesu. Mulungu anatuma Mwana wace ku dziko lapansi[23]. Yesu anaonetsa cifundo ca kwa anthu. Anawasamalira. Anawafera ngakhale pa mtanda[24]. Imfa yake inali njira yeniyeni kuti macimo anathe kukhululukidwa[25]. Ici cionetsa coipa ca macimo! Aliyense amene adalira pa Yesu yekha pa cipulumutso cake, akhululukidwa ndithu. Munthuyo asanduka mwana wa Mulungu[26] ndipo adzamvera nikukhala naco cisamaliro capadera ca kwa anthu a Mulungu[27]. Ciriconse cimene cicitika m’miyoyo yao ciwapindulitsa[28].
Wosamalira wanzeru
Mulungu adziwa zimene ziri zabwino zoposa[29]. Alamulira ndi nzeru[30]. Afuna kukonza zonse momwe zinali pa nthawi yamene Adamu ndi Hava analibe kucimwa. Afuna anthu kumumvera ndi kumulemekeza[31]. Miyoyo yathu ipezeka m’dongosolo la Mulungu la kukonza zonse kuti zikhala kwa ulemerero wake[32]. Sitikhoza kumvetsa zonse za dongosolo lake. Nthawi zina zinthu zabwino zicitika m’miyoyo yathu, monga kukolola kwabwino, ukwati kapena kukhala ndi cakudya ndi zobvala. Tiyenera kuyamikira Mulungu amene atipatsa madalitso awa[33]. Nthawi zina zinthu zoipa zicitika. Ngati ziri tero, tiyenera kukhala odekha ndi osadandaula[34]. Mulungu salakwa. Tiyenera kumkhulupirira pa nzeru zake.
Wosamalira wokhulupirika
Nthawi zambiri kukhulupirira Mulungu ndi kobvuta, makamaka pa nthawi ya mabvuto. Kukomana ndi mabvuto kungatipangitse kuganiza kuti Mulungu sasamalira kapena kuti salamulira.
M’Baibulo tiwerenga zitsanzo zambiri za anthu amene anabvutika. Angakhale tero, iwo anapirira kukhulupirira Mulungu pa ubwino wake, mphamvu yake, cisomo cake ndi nzeru zake.
Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango pa kusaleka kupemphera[35]. Hana anasekeredwa pa kusabala mwana[36]. Yobu anafa ana ake onse, anataya zinthu zonse nadwala[37]. Mfumu Hezekiya anadwala nakhala pafupi pa kumwalira[38]. Mose ananyozedwa ndi anthu amene iye anapulumutsa ku ukapolo[39]. Stefano anaphedwa pa kuulula Yesu kukhala Mpulumutsi wake[40]. Paulo anazunzidwa nalangidwa pa kulalikira Yesu[41]. Abale a Yosefe anamgulitsa kwa anthu a dziko lina[42]. Adani a Nehemiya anafuna kumupha pokonza zipupa za Yerusalemu, mzinda wa Mulungu[43].
Anthu awa ndiwo citsanzo kuli ife. Iwo anapfuulira Mulungu ndipo sanataye cikhulupiriro cao mwa Mulungu wabwino, wamphamvu, wacifundo ndi wanzeru[44]. M’zowawa zao, iwo anadzipereka kwa Mulungu. Anakana kugwirizana ndi uchimo. Nthawi zina Mulungu anawapulumutsa. Nthawi zina Mulungu sanapatse anthu ake zimene iwo anampempha, pakuti Iye anali ndi dongosolo labwino kuposa.
M'Baibulo tiwerenga nthano ya amuna amene anapirira ndi kudzipereka kwa Mulungu[45]. Iwo anauzidwa kugwadira fano, koma anakana kucita tero. Mfumu inawauza kuti ngati sadzagwadira, iwo adzaponyedwa m’moto namwalira. Amunawo anayankha kuti Mulungu ali ndi mphamvu kuwapulumutsa, ‘Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo’[46]. Anafuna kumvera Mulungu yekha, angakhale adzafa cifukwa ca kukana.
Conco, pa nthawi ya mabvuto, khulupirirani Mulungu, pirirani ndipo kanani kucimwa[47]. Khalani otsimikiza kuti Mulungu sadzasiya anthu ake nthawi zonse[48]. Iye atatsiriza dongosolo lake m’miyoyo yao, adzawatenga naye Kumwamba. Sadzawasiya nthawi zonse, pakuti Iye ndi wokhulupirika[49].
Wosamalira wolungama
Pamene Yesu adzabweranso adzaweruza anthu onse[50]. Adzalekanitsa anthu ake ndi amene si ali ake[51]: iwo amene anamlandira kukhala Mbuye wao ndi iwo amene sanamlandire. Ciweruzo cake cidzakhala moyenerera ndi cosabwerezeka[52]. Iwo amene si ake, adzakhala m’Gehena muyayaya, kopanda cisamaliro ca Mulungu[53]. Ngati mukalibe kukhala m’modzi wa anthu ake, lapani macimo anu ndipo pemphani Yesu Mpulumutsi kukupulumutsani ku macimo anu[54]. Aliyense amene ali wake adzakhala Kumwamba muyayaya kulemekeza Iye amene anawasamalira nthawi zonse mwa cisomo[55].
~
Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa – Mateyu 10.22
------------------------------------------------------------------------------
[1] Akolose 1.17, [2] Genesis 1 ndi 2, [3] Salimo 119.68, Salimo 100.5, [4] 1 Mbiri 29.11, Salimo 97.9, [5] Genesis 1.27, [6] Genesis 1.21, Salimo 104.24, [7] Genesis 2.9, Genesis 2.15-17, [8] Genesis 3.8, [9] Genesis 2.16 ndi 17, [10] Salimo 93.1 ndi 4, Salimo 103.19, [11] Salimo 135.6, Yesaya 43.13, [12] Salimo 89.6 ndi 9, Salimo 91.10, Yesaya 14.27, Miyambo 21.1, Yobu 1.12, [13] Aefeso 1.11, Miyambi 19.21, Miyambi 16.33, [14] Genesis 3.6, [15] Genesis 3.14-19, Aroma 3.19, [16] Genesis 6.5, Marko 7.21-23, Yeremiya 17.9, Aroma 1.30 ndi 31, Salimo 14.1-3, [17] Afilipi 2.21, 1 Samueli 4.3, Numeri 23.27, [18] Yakobo 3.2, Aroma 3.11, [19] Yesaya 57.15, Yesaya 59.2, Yohane 3.36, Ezara 9.15, [20] Aroma 3.20, [21] Akolose 1.17, Macitidwe a Atumwi 17.24-28, Salimo 65.9-13, Salimo 104.14, Yobu 37.6-13, [22] Salimo 145.16, Mateyu 5.45, [23] 1 Yohane 4.9, 1 Yohane 4.14, [24] Mateyu 27, [25] 2 Akorinto 5.21, Yohane 3.14-16, Agalatiya 3.3, [26] Yohane 1.12, Agalatiya 3.26, [27] Mateyu 10.29, Aroma 8.32, [28] Aroma 8.35-39, 2 Akorinto 5.1, Ahebri 12.6-8, Yakobo 1.3-4, [29] Salimo 92.5, [30] Yesaya 28.29, Salimo 145.3, [31] Yesaya 45.22 ndi 23, Yesaya 43.19, Mika 6.8, [32] Aefeso 1.9-11, Yeremiya 9.24, [33] Deuteronomo 8.10, [34] Aroma 5.3, Salimo 39.9, Danieli 4.35, [35] Danieli 6, [36] 1 Samueli 1.6, [37] Yobu 1 ndi 2, [38] 2 Mafumu 20.1, [39] Eksodo 15.24, [40] Macitidwe a Atumwi 8, [41] 1 Akorinto 4.11-13, [42] Genesis 37.28, [43] Nehemiya 6 ndi 7, [44] Salimo 55.23, Aroma 8.18, [45] Danieli 3, [46] Danieli 3.18, [47] Deuteronomo 31.8, Salimo 73.26, Afilipi 4.6, [48] Yakobo 1.12, [49] Salimo 125.2, Yesaya 41.10, Yakobo 1.12, [50] 2 Timoteo 4.1, [51] Mateyu 25.31-33, [52]Salimo 96.13, [53] Cibvumbulutso 20.15, [54] Marko 1.15, Salimo 25.7, Macitidwe a Atumwi 20.21, [55] Cibvumbulutso 7.16-17, 2 Akorinto 5.1, Salimo 145.1, Yohane 10.28-30