top of page
Afbeelding22_edited.jpg

KUTHANA NDI MATENDA

Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa: Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga. Ambuye, cikhumbo canga conse ciri pamaso panu; Ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu – Masalimo 38.8 ndi 9


Ndipo adzawaputukira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita – Cibvumbulutso 21.4


Nthawi zambiri timamva za matenda. Malungo, bipi, tizilombo, stroko, kansa ndi matenda ena amabvutitsa ife ndi anzathu. Cifukwa ca ici tingafunse mafunso, monga awa:

  • Ndi cifukwa ciani nadwala? Kodi nacimwa?

  • Tinapempha Mulungu kuti aciritse mnzathu, koma adwalabe

  • M’cipangano cakale Mulungu anacenjeza anthu asanaononge. Ndi cifukwa ciani sacita tero masiku ano?

  • Anthu ambiri a m’banja langa adwala. Ndi ciani cimene cicitika?

  • Mnzanga wapafupi samapita ku calichi ndipo akhala ndi moyo wabwino koma akristu aoneka monga amabvutika kwambiri.

Nthawi zina matenda amatsatanatsatana ndipo sitikwaniritsa kuyankha mafunso. Tidera nkhawa, tikumva monga osowa ndi otayika. Anthu ena amaganiza kuti kufa ndi kwabwino kuposa kukhala ndi mabvuto.

Baibulo litiuza za anthu amene anakhala nazo zinthu cimodcimodzi monga ife. Anali ndi mafunso monga ife tili nao. Tiyeni tione zimene Baibulo litiuza za kuthana ndi matenda.  


Ciyambi ca matenda

Mitu yoyamba ya m’Baibulo itiuza kuti Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi [1]. Zonse zinali mu mgwirizano wabwino: Mulungu, anthu ndi cilengedwe conse.

M’Genesis 3 tiwerenga zimene zinacitika patapita nthawi ya kulenga: Adamu ndi Hava, anthu oyamba olengedwa ndi Mulungu,  sanamvere Mlengi wao[2]. Kucokera nthawi iyo zonse zasinthika[3]: dziko ndilo tembereredwa cifukwa ca chimo[4]. Zinthu zoipa zonse m’umoyo wathu ndizo zotsatira za temberero limene litsatira ku imfa[5], mwacitsanzo ubwenzi ndi Mulungu uonongeka, mjedo, matenda, kudana, njoka zoluma komanso udzudzu umene utipereka matenda a malungo.

Dziko lonse ndilo tembereredwa  ndi Mulungu; munthu aliyense angadwale. Ngakhale ndinu osauka kapena olemera, ophunzira kapena osaphunzira: m’umoyo wanu mudzakhala ndi matenda ndipo tsiku lina mudzafa[6]. Kudwala kutikumbutsa chimo loyamba m’Paradaiso.


Mulungu ndiye wolamulira

Ngakhale zonse zasinthika cifukwa ca chimo loyamba m’Paradaiso, Mulungu sanasanduke. Amasamalirabe cilengedwe cake[7]. Alamulira: kulibe kanthu kalikonse komwe kacitika mwadzidzidzi kapena mwa mwayi[8]. Mulungu amasamalira ndi kuteteza zolengedwa zonse.

Kulingana ndi Baibulo ndi comveka kuti Mulungu si ndiye obweretsa macimo ndi zotsatira zake. Komabe m’Baibulo tiwerenga zitsanzo zambiri kuti Wolamulira wamphamvu zonse amagwiritsa nchito macimo ndi zotsatira zake kuti akwaniritse colinga cake: ulemerero wake. Tiganizireko zitsanzo zina za m’Baibulo:

  1. Aisrayeli anacimwira Mulungu m’cipululu: analankhula motsutsana naye[9]. Cifukwa ca ico Mulungu anawalanga ndi njoka. Anthu ambiri analumidwa nadwala ndi kufa. Aisrayeli anazindikira kuti ayenera kulapa ku macimo ao. Mulungu agwiritsa nchito mabvuto monga matenda kukalanga mitundu cifukwa ca kusamvera kwao ku makhalidwe ndiponso kuti imvetsetse kuti ifunika Mulungu[10].

  2. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi ophunzira ake anamfunsa kuti ndi cifukwa ciani mwamuna uyu ndiye wosapenya[11], ‘Kodi ndi iye wocimwa kapena makolo ake?’ Yesu anawauza kuti mwamunayo sanali wosapenya cifukwa ca colakwa ciriconse koma kuti mphamvu ya Mulungu ionetsedwe. Cimodzimodzi ndi Lazaro, mnzake wa Yesu, amene anadwala[12]. Yesu anayembekeza. Sanapite msanga kukamuona mpaka atafa cifukwa anthu  anafunika maphunziro ake a Iye yemwe kuti alemekeze Mulungu. Mulungu agwiritsa nchito mabvuto monga matenda kutiphunzitsa cina cake cimene tiyenera kudziwa za ife tokha kapena za Mulungu[13].

  3. Yobu anali munthu woopa Mulungu[14]. Komabe anataya  zonse zimene zinali zake: ana ake, cuma cake ndiponso thanzi. M’nzeru zake Mulungu analola Satana kubvutitsa Yobu m’njira iyo, koma moyo wake asaukhuze. Mulungu anagwiritsa nchito zosautsa izi kuti ayese cikhulupiriro ca Yobu. Mulungu agwiritse nchito mabvuto monga matenda kutiyesa kukaona ngati tipirira kumkhulupirira m’zocitika zonse[15]

Zitsanzo izi zitionetsa njira zosiyanasiyana m’mene Mulungu wamphamvu zonse ndi wopambana agwiritsa nchito matenda m’umoyo wathu ku ulemerero wake umene ndiwo colinga ceniceni ca cilengedwe. Komabe ndi cotheka kuti sitikwaniritsa kuyankha mafunso, cifukwa ndi Mulungu yekha amene adziwa zonse[16]. Mulungu adziwa zimene ziri zabwino zoposa[17]. Cifukwa ca ici tiyenera kupirira m’zowawa[18] ndi kuyamika Mulungu pamene tipita m’tsogolo[19]. Ngati Mulungu ndiye Atate wanu mwa Yesu, simunenera kudera nkhawa za tsogolo[20]: cifukwa ca cisamaliro ndi citetezo cake pa inu zinthu zonse zigwirizana ndipo mudzamlemekeza nthawi zonse[21].


Ufumu wa Mulungu

Pamene Yesu, Mwana wa Mulungu, anali pa dziko lapansi anaciritsa anthu ambiri ndipo anafa pa mtanda kusenza temberero la uchimo wa ana ake[22]. Cifukwa ca ici ana a Mulungu adzaloledwa kukhala naye Kumwamba nthawi zonse. Kumwamba zonse  zili m’mgwirizano wabwino monga zinali pa nthawi ya kulenga[23]: uko kulibe matenda, imfa ndi chimo.

Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudzakomana ndi matenda m’umoyo wanu wa pa dziko lapansi[24], koma kumbukirani kuti Mulungu ndi wamphamvu zonse ndipo agwiritsa nchito matenda ku ulemerero wake[25]. Muyembekezere kukhala naye Kumwamba kumene kulibe nthenda iliyonse imene ingakubvutitseni[26].

Ngati si ndinu mwana wa Mulungu pa nthawi iyi, simudzakhala Kumwamba, pokhapokha mukalapa ku macimo anu ndi kudalira pa Yesu pa cipulumutso cake. Ngati simudzapulumutsidwa pa nthawi ya imfa yanu, mudzakhala ku Gehena pamodzi ndi Satana kwa nthawi zonse[27]. Yesu afuna ndipo akhoza kukwaniritsa kukupulumutsani ku temberero la uchimo[28]. Anaphunzitsa ici mwa zodabwitsa zimene anacita: Iye ndiye Mwana wa Mulungu amene  analonjezedwa kubwera kukapulumutsa anthu ku macimo ao[29].

Kodi tiyenera kuthana bwanji ndi matenda?

Tiganizire za kuthana ndi matenda m’njira yotani kulingana ndi Baibulo.

  • Pemphani thandizo kwa Mulungu. Baibulo litionetsa zitsanzo za anthu obvutika amene anapempha Mulungu[30]. Mulungu anawayankha m’njira yabwino yoposa kulingana ndi Iye. Khulupirirani Mulungu kuti adziwa zimene ziri zabwino zoposa za ife ndipo mlemekezeni nthawi zonse[31].

  • Mukadwala muganizire umoyo wanu ndipo mudzifunse ngati Mulungu akulangani cifukwa ca chimo limene mwacita. Ngati inde, ululani chimolo ndipo lapani[32]. Ngati simudziwa, musayese kupeza cifukwa ndipo mudzipereke kwa Iye. Musauze anthu ena kuti adwala cifukwa ca chimo limene acita, cifukwa mungaweruze moipa msanga[33].

  • Kudziteteza, kukhala ocenjera ndi kupita ku cipatala kukapeza thandizo ndiko kwabwino kulingana ndi Baibulo ndiponso sikutsutsa kukhulupirira Mulungu[34], koma si njira zonse zimene ziloleka[35]. Dziwani kuti kudalira pa kanthu kalikonse kuposa kudalira pa Mulungu ndi chimo.

  • Kufooka sikutsutsa Mulungu[36]. M’Baibulo muli zitsanzo kuti Mulungu anasankha anthu ofooka ku ulemerero wake.

  • Kumbukirani kuti Yesu anazunzidwa pa dziko lapansi cifukwa ca ana ake. Adziwa zowawa zao pamene abvutika ndipo ndiye wacifundo[37].

  • Khalani okonzeka pa nthawi ya imfa yanu[38]. Iwo okha amene adalira pa Yesu yekha (kwa cipulumutso ndi zofunika zao zonse) ndiwo okonzeka[39].

  • Yamikani Mulungu pamene mukhala athanzi ndipo thandizani odwala[40]. Baibulo litilimbikitsa kuti tisamalire anthu ofunika thandizo.


~

Ndidze pafupi pa Mlungu wanga,

Ngakhale pamtanda mundikweza;

Koma ndiyimbabe, Mbuye mndikhalitse,

Mbuye mndikhalitse m’fupi Ndinu.

~

---------------


[1] Genesis 1 ndi 2, [2] Genesis 3.6, [3] Genesis 3.14-19, [4] Genesis 3.17, [5] Aroma 5.12, [6] Ahebri 9.27, [7] Ahebri 1.3, Salimo 104.5-15, [8] Mateyu 28.18, Salimo 66.7, Miyambo 16.9, [9] Numeri 21.4-9, [10] Eksodo 15.24, 2 Atesaloniki 1.8, Macitidwe a Atumwi 5.1-10, Deuteronomo 28, [11] Yohane 9, [12] Yohane 11.1-6, [13] 2 Akorinto 4.7, [14] Yobu 1, [15] 1 Petro 1.7, Yakobo 1.2-12, Salimo 66.10, [16] Deuteronomo 29.29, Yobu 15.8, [17] Aroma 8.28, [18] Aroma 5.3, [19] Deuteronomo 8.10, [20] Cibvumbulutso 2.10, [21] Mateyu 6.25-34, Salimo 55.22, 1 Petro 1.6-9, [22] Agalatiya 3.13, [23] Cibvumbulutso 21.4, [24] Afilipi 1.29, [25]Ahebri 2.10, Ahebri 12.6-11, 1 Petro 4.13, [26] Aroma 8.18, [27] Mateyu 13.50, [28] Luka 13.34, [29] Luka 4.41, Yohane 20.30 ndi 31, Mateyu 19.11, [30] Yesaya 26.16, Marko 5.23, Luka 5.12, [31] 1 Akorinto 10.13, Aefeso 5.20, [32] 1 Yohane 1.9, [33] Yobu 42.7, [34] Miyambo 22.3, Genesis 41.36, Mateyu 9.12, [35] Levitiko 19.31, [36] 2 Akorinto 12.9 ndi 10, [37] Ahebri 4.15, Yesaya 53.3, 2 Akorinto 1.5, [38] Yesaya 38.1, [39] 1 Yohane 5.12, [40] Agalatiya 6.2

bottom of page