Tsiku la Good Friday ndi Tsiku la Paska
Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu – Yohane 19.30
Ambuye anauka ndithu – Luka 24.34
M’mudzi wina munali mnyamata. Dzina lake ndiye Chisomo. Makolo ake anali ndi nkhuku za cakudya ndi malonda. Chisomo anakonda nkhuku, makamaka tiana ta nkhuku tating’ono. Tate wa Chisomo anamuuza kusankha kamwana kamodzi kuti kakhale kake. Chisomo anasanka kamene anakonda kwambiri: kamodzi kang’ono ka cikasu kamene kanali ndi mapiko ofiira. M’madzulo onse pamene Chisomo anadzithamangitsa kukadzilowetsa m’khola kuona kamwana ka nkhuku kake podziwa kuti kali bwino. Sanafune munthu wina aliyense kudziwa koma anapatsa kamwana ka nkhuku kake dzina; Mphatso.
Usiku wina kunada kwambiri ndipo kunalibe phokoso m’mudzi. Anthu onse anagona. Mwadzidzi Chisomo anauka. Anamva nkhuku zikucita phokoso, lina limene anazindikira msanga: moto! Chisomo anautsa tate wake ndipo anatenga kanyali kang’ono. Anathamanga ku nyumba ya nkhuku nayamba kuzimitsa moto. Chisomo anapfuula, ‘Kamwana ka nkhuku kanga! Sindifuna kuti kafe!’
Atazimitsa moto Chisomo ndi tate wake anasakira nkhuku. Koma kunalibe ciyembekezo ciriconse: nkhuku zonse zidafa m’moto. Chisomo analira, ‘Kamwana ka nkhuku kanga!’ Mwadzidzidzi anamva liu laling’ono, PEEP, ndipo anadzindikira kumene liu linacokera: munsi mwa phiko la mai wa Mphatso kanthu kakang’ono kanayenda pang’ono. ‘Mphatso!’, Chisomo anapfuula, ‘Mphatso akhala ndi moyo!’ Mphatso inatetezeka munsi mwa phiko la mai wake.
‘Ndi codabwitsa, iai?’, anati tate kwa Chisomo. Nkhuku inafa kuti kamwana ka nkhuku kako kakhale ndi moyo. Inapatsa moyo wake kukateteza kamwana kwake. Codabwitsa!’ Tsiku ilo Chisomo sanaleke kusekerera.
M’Baibulo tiwerenganso nthano yodabwitsa: Yesu, mwana wa Mulungu, anafa pa mtanda ndipo anauka kwa akufa kupulumutsa anthu ocimwa.
Yesu anafa pa mtanda: tsiku la Good Friday
Yesu anabadwa pa dziko lapansi monga mwana[1]. Ici timakumbukira pa tsiku la Krismasi. Pa nthawi ya umoyo wake anthu ambiri anakonda kuona zodabwitsa zimene Yesu anacita monga kuciritsa odwala, kucurukitsa cakudya ndi kuukitsa akufa. Yesu sanacite coipa ciriconse. Sanalakwe: anali wokoma mtima, wacifundo ndi wacikondi kwa anthu onse. Anaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu[2] ndipo anafotokoza kuti ubwenzi wa anthu alionse ndi Mulungu watsiridwa cifukwa ca chimo limene ndilo kusayeruzika[3]. Ananena kuti Iye yekha amene adadza kupereka moyo wake dipo ndi njira yokhala m’ubwenzi wabwino ndi Mulungu[4].
Ngakhale anthu ambiri anakonda kuona Iye pocita zodabwitsa, ena ambiri sanakonde uphunzitsi wake. Iwo anati kuti Yesu anacitira Mulungu mwano mwa kunena kuti ndiye mwana wa Mulungu[5]. Sanakhulupirire zimene Yesu ananena. Makamaka anthu a cipembedzo m’masiko awo sanafune kumva kuti njira yeniyeni yopulumutsidwa ndi mwa Yesu osati mwa zocita zathu.
Anthu awa anada Yesu tere kuti anafuna Yesu aphedwe[6] ndipo zimene zinacitika ndi izi[7]: m’modzi wa ophunzira ake amene adayenda naye nthawi yaikulu anampereka kukamangidwa.
Anaperekedwa kwu Kayafa (mtsogoleri wa anthu a cipembedzo) kuti aweruze Yesu. Kayafa anaweruza kuti Yesu ndiye wolakwa cifukwa ca kunena kuti ndiye mwana wa Mulungu. Anapereka Yesu ku Pilato kazembe amene anaweruza kuti Yesu sanalakwe. Koma cifukwa ca kupanikiza kwa gulu Yesu anazunzidwa ndi kuperekedwa ku Golgota kumene anapacikidwa.
Yesu sanadabwitsidwe ndi zimene zinacitika cifukwa zonse zinali m’cifuniro ca Mulungu[8]. Yesu adadza pa dziko lapansi kupulumutsa ocimwa mwa kuwafera pa mtanda[9]. Mwa cikondi anasiya ulemerero wake Kumwamba kuti akhale wosabvala pa mtanda ndiponso kuti afe[10]. Ndi kusiyanitsa kwakukulu!
YESU ANADZIKHUTHULA[11]
Imfa ya Yesu ndi yofunikira kwambiri kwa umunthu cifukwa Iye yekha ndiye njira yopulumutsidwiramo ku chimo[12]. Baibulo likamba kuti anthu onse ndiwo ocimwa[13]. Mulungu akuda chimo, ndiye kulibe munthu amene adzalowa Kumwamba pokhapokha ngati macimo ake acotsedwa[14]. Uthenga wabwino ndi kuti sitiyenera kudzipulumutsa. Cimene ciri cofunikira cabe ndi kulapa ku macimo ndi kukhulupirira Yesu pa cipulumutso[15]. Kwinaku cikhulupiriro ndi kulapa moonadi si zinthu zimene tiyenera kukwaniritsa koma zipatsidwa ndi Mulungu mwa cisomo[16]. Ndiye Mulungu angatipatse zonse zimene tifunika kuti tipulumuke mwa Yesu amene anafa pa mtanda cifukwa ca ocimwa monga ife. Kumbukirani nkhani ya Chisomo ndi kamwana ka nkhuku kwake. Tawerenga kuti nkhuku imodzi inafa kukapulumutsa mwana wake. Yesu anafa m’malo mwa anthu ake kuti iwo akhale nawo moyo wosatha ndi Mulungu Kumwamba. Uthenga wabwino uwu ndi umene timakumbutsidwa pa tsiku la Good Friday.
Yesu anauka kwa akufa: tsiku la Paska
Patapita masiku atatu atafa Yesu anauka kwa akufa[17]. M’mawa, kusanayambe kuca, kunali cibvomezi ndipo mngelo anatsika Kumwamba amene anati kuti Yesu adauka kwa akufa.
YESU AKHALA NDI MOYO![18]
Kuuka kwa Yesu ndi kofunikira kwambiri monga kufa kwake. Kuuka kwake ationetsa kuti imfa, ndiyo mphotho ya uchimo[19], inagonjetsedwa ndi Yesu cimene citanthauza kuti anagonjetsanso chimo. Yesu ndi wamphamvu woposa chimo ndipo sitiyenera kucita kalikonse kucotsa macimo athu cifukwa Yesu anacita zonse kale. Anazicita kamodzi kusenza macimo a ambiri amene amkhulupirira[20].
Ngati mwalapa ndi kukhulupirira Yesu, Mulungu akutsimikizirani umoyo wosatha[21]. Nthawi zambiri Baibulo litsimikizira okhulupirira kuti ndiwo mu Yesu[22]. Iye akhala ndi moyo, ndiye omkhulupirira akhalanso ndi moyo ndi moyo wosatha. Ganizirani za citsanso ca munthu amene agwa m’madzi. Ngati mutu wake siri m’madzi adzapema bwino ndipo sadzamira m’madzi. M’Baibulo Yesu acedwa Mutu[23] ndiye iwo amene amkhulupirira akhala ndi moyo wosatha cifukwa Yesu akhala ndi moyo. Kuuka kwa Yesu ndiko uthenga wabwino. Caka ciriconse pa tsiku la Paska timakumbukira zodabwitsa za kuuka kwa Yesu.
Kufa ndi kuuka kwa Yesu m’masiku onse
Ambiri a ife tidziwa nthano ya kufa ndi kuuka kwa Yesu. Koma mumvetsetsa zimene zinacitika kodi? Kodi kufa ndi kuuka kwa Yesu kumatanthauzanji m’umoyo wanu wa masiku onse? Yesu ayenera cikhulupiriro cathu. Ngati simunapereke umoyo wanu kwa Iye mpaka lero, lapani ndi khulupirira Yesu cifukwa kopanda Iye ndinu otayika opanda moyo wosatha[24]. Kumbukirani kuti ndiye wacifundo. Adzapulumutsa inunso ngati mupita ndi kudalira pa Iye pa cipulumutso[25]. Pemphani Mulungu cifundo cake.
Mukadziwa kuti Yesu anafa ndi kuuka cifukwa ca inu, mtumikireni masiku onse[26]. Kumbukirani kuti muli ndi citsimikizo ca umoyo wosatha cifukwa ca kuuka kwa Yesu. Alondolereni m’zonse[27]. Osataya ciyembekezo [28]ca pa moyo wanu ndi moyo wosatha cifukwa Yesu anagonjetsa chimo ndi imfa. Werengani Baibulo lanu kukaphunzira zina zambiri za Iye ndipo mlemekezeni pa zonse zimene anakucitirani.
~
Ulemu kwa Mlungu, Ambuye wathu,
Akonda, ‘napatsa ‘fe mwana wace;
Napatsatu moyo kuombola ‘fe,
Pa khomo la moyo natsegulatu.
Tamani Mbuyeyo, dziko limvere ‘Ye
Tamani Mbuyeyo, anthu akondwetu;
Idzani kwa ‘Tate mwa mwana wace,
M’patseni ulemu, anakonda ‘fe.
~
Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo - 1 Akorinto 15.3 ndi 4
---------------------
[1] Luka 2.6-14, [2] Mateyu 13, Yohane 3.5-6, Yohane 8.19, [3] 1 Yohane 3.4, [4] Yohane 14.6, Mateyu 20.28, [5] Mateyu 9.3, [6] Yohane 11.53, [7] Mateyu 27 ndi 28, [8] Mateyu 20.18-19, [9] Luka 5.32, [10] Yohane 3.17, 1 Yohane 4.9-10, [11] Afilipi 2.6-8, [12] Macitidwe a Atumwi 4.12, 1 Timoteo 2.5, [13] Aroma 3.23, [14] Yesaya 33.24, Yohane 3.3, [15] Marko 1.15, 2 Akorinto 5.21, 1 Petro 2.24, [16] Aefeso 2.8, Aroma 5.16, [17] Mateyu 28.1-7, [18] Marko 16.6, Luka 24.6, [19] Aroma 6.23, [20] Ahebri 9.28, [21] Yohane 10.28-29, Yohane 11.25-26, [22] 1 Yohane 4.15, [23] Aefeso 4.15, [24] Aroma 10.9, 1 Yohane 5.12, Yohane 3.36, [25] 1 Yohane 1.9, [26] Aroma 6.5-6, [27] 2 Akorinto 5.15, Luka 9.23, [28] 1 Petro 1.3