top of page
Uthenga wabwino Krisimasi.jpg

UTHENGA WABWINO WA CIKONDWERO CACIKULU

Kubadwa kwa Yesu

Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikulu, cimene cidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye – Luka 2.10 ndi 11


Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera – 2 Akorinto 8.9


Citsanzo ca kudzicepetsa

Kale kunali banja lolemera kwambiri. Iwo anakhoza kugula kalikonse komwe anafuna. Onse a m’banja anaoneka okongola. Banja silinayenere kudera nkhawa ciriconse. Anasangalala umoyo. Banja lolemera anathandiza anthu osauka mwa kuwapatsa zimene anasowa. Tsiku lina mwana m’modzi wa banja lolemera anaganiza za kusiya banja lake ndi kukhala ndi osauka. Iye anasanduka m’modzi wa osauka.

Kodi mungayerekeze munthu wosiya banja lake lolemera kuti akhale m’modzi wa osauka? Ndico kudzicepetsa kwakukulu!

Baibulo litiuza za Wina amene anadzicepetsa: Yesu. Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. Anasiya Kumwamba nabadwa pa dziko lapansi. Mfumu wamphamvu zonse anakhala Khanda wopanda mphamvu. Mwini wa zonse anakhala Mwamuna wamba. Anadzicepetsa kupangitsa anthu ocimwa kukhala ana a Mulungu. Ndi codabwitsa kwambiri!


Asanabadwe Yesu

Mbali yoyamba ya m’Baibulo ichedwa Cipangano cakale. Itiuza zimene zinacitika asanabadwe Yesu pa dziko lapansi. M’Baibulo tiwerenga kuti Mulungu analenga zonse. Zonse zolengedwa ndi Iye zinali bwino[1]. Mulungu analenganso Adamu ndi Hava, ndiwo anthu oyamba. Iwo anali abwenzi a Mulungu.

Satana, mdani wa Mulungu, sanakondwere poona iwo okondwera. Anafuna kuononga ubwenzi pakati pa Mulungu, anthu ndi cilengedwe conse. Satana anati kuti Mulungu adanama: anthu adzafa atadya mtengo koma adzakhala monga Mulungu, ngakhale Mulungu anawaletsa kucita tero[2]. Iwo awiri Adamu ndi Hava anadya cipatso ca m’mtengo[3]. Sanamvere Mulungu. Kusamvera ndi chimo[4]. Chimo linyoza Mulungu[5].

Zonse zinasinthidwa pamene Adamu ndi Hava sanamvere. Matenda, ndeu, imfa ndi mabvuto ena onse ndiwo zotsatira za chimo limene Adamu ndi Hava anacita. Dziko lonse lapansi ndi lotembereredwa[6]. Cotsatira cina ca chimo loyamba ndi cakuti ubwenzi pakati pa Mulungu ndi anthu onse ndiwo woonongeka[7]. Ico cichedwa umphawi wa m’mzimu; anthu onse ndiwo ocimwa: otayika kopanda Mulungu ndiponso olephera kumtumikira[8]. Tiyenera kukhala ku Gehena kutali ndi Mulungu nthawi zonse.

Zonse zasinthika, koma Satana sanakhoze kupambana Mulungu[9]. Mwa cikondi, Mulungu analonjeza kutuma Mwana wake Yesu ku dziko lapansi[10]. Iye adzacotsa temberero la Mulungu pa macimo a anthu ake[11].


Kubadwa kwa Yesu

Zaka zambiri zitapita nthawi ya chimo loyamba, Mulungu anatuma  mngelo kwa Mariya. Mngelo anamuuza kuti adzakhala ndi Mwana: Yesu[12]. Mulungu Mzimu Woyera adzapanga thupi la Yesu. Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. Mulungu Atate ndiye Tate wa Yesu.

Yesu anabadwa m’khola[13]. Kunalibe malo abwino kuti anabadwako. Kunalibe munthu amene anadziwa za kubadwa kwa Mwana wa Mulungu pa dziko lapansi. 

Mulungu anafuna kuti anthu ena adziwe za kubadwa kwa Yesu. Anatuma mngelo wake kuti auze abusa ena za kubadwa kwa Yesu[14]. Abusa anali anthu wamba, komabe ndiwo oyambirira kumva kwa kubadwa kwa Yesu.  Kubadwa kwa Yesu kunali uthenga wabwino. Angelo anaimba[15]:

Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,

Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

Abusa anakondwera kwambiri. Anafalitsa uthenga wabwino kwa

anthu onse. Anzeru a kum’mawa anabwera kuona Yesu. Anampembedza monga Mfumu wao[16]. Anakondweranso.

Mfumu Herode sanakondwere[17]. Sanafune Yesu kukhala Mfumu. Anafuna kupha Yesu. Ico sicinacitike, cifukwa Mulungu anateteza Yesu. Mulungu anafuna Yesu kupulumutsa anthu otayika opanda Mulungu cifukwa ca macimo ao[18].


Ndi cifukwa ciani kubadwa kwa Yesu ndiko uthenga wa cikondwerero cacikulu?

Baibulo likamba kuti anthu onse ndiwo ocimwa amene alephera kumvera Mulungu[19]. Onse ndi otayika kopanda Mulungu: ndife osauka m’mzimu. Ocimwa sakhoza kulowa Kumwamba pokhapokha ngati macimo ao acotsedwa[20]. Timalephera kucotsa macimo athu, ngakhale tiyesadi. Sitikhoza kudziyeretsa ku macimo athu[21]. Kulibe munthu wina amene akwaniritsa kutiyeretsa ku macimo athu. Tifunika wina wopanda uchimo ndiponso wamphamvu kuposa uchimo kuti acotse macimo athu.

Munthuyo wopanda uchimo ndi wamphamvu ndiye Yesu![22]

Yesu, Mwana wa Mulungu, ali ndi mphamvu yotiyeretsa ku macimo athu ndipo afuna kucita tero. Anali munthu kuti afe pa mtanda. Mwa kufa pa mtanda anaombola anthu ake ocimwa ku macimo ao[23]

Kubadwa kwa Yesu ndiko uthenga wa cikondwerero cacikulu potionetsa kuti Mulungu anapanga njira yobweretsanso ocimwa m’ubwenzi  wake. Yesu yekha ndiye Nkhoswe pakati pa Mulungu ndi anthu pakuti Iye ndiye Mulungu komanso Munthu[24].


Kukumbikira kubadwa kwa Yesu masiku onse

Caka ciriconse timakumbukira kubadwa kwa Yesu pa tsiku la  Krisimasi. Komabe, tingakumbukire kubadwa kwake pa tsiku lirilonse. Munsi muli mfundo zimene zingakuthandizeni kuganizira za kubadwa kwa Yesu:

1.   Yesu anakhala Munthu monga ife, koma wopanda chimo[25]. Adziwa za kumva njala, kudwala kapena kukhala yekha. Akhoza ndipo afuna kutithandiza m’zonse zimene zikomana nazo.

2.   Yesu anadzicepetsa mwa kubadwa kwake pa dziko lapansi[26]. Tizidzicepetsanso pa maso pa Mulungu ndi anthu ena.

3.   Cifukwa ca Yesu anthu ocimwa akhale ana a Mulungu[27]. Yesu anadzicepetsa kubweretsa anthu ake ku ulemerero wa Kumwamba. Tiyenera kudziwa Yesu monga Mpulumutsi wathu[28].

4.   Ngati mudziwa kuti muli opanda Mulungu, funsani Yesu kukuyeretsani ku macimo anu. Afuna kupulumutsa inu[29]. Lapani ku macimo anu ndipo dalirani pa Iye yekha pa cipulumutso cake[30].

5.   Ngati mudziwa kuti Yesu akupulumutsani ku macimo anu, citani ciriconse cimene cimkondweretsa. Werengani Baibulo kuphunzira zina zambiri za Iye. Falitsani uthenga wabwino wa cikondwerero cacikulu. Monga munthu wa Kumwamba[31], lemekezani Mulungu nthawi zonse. 


~

Kale m'mzinda wacifumu

Munalimo m'kholamo.

Momwe mkazi anaika

Mwana wake m'ndyeromo.

Ndiye mkaziyo Mariya

Yesu Kristu Mwanayo


Uyu 'natsikira kuno,

Mlungu Mbuye wathuyo.

Anabadwa uyu m'khola

Anagona m'ndyeromo.

Mwa osowa ndi oipa,

Yesu anakhalamo.

~


Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye – 1 Yohane 4.9

--------------------

[1] Genesis 1 ndi 2, [2] Genesis 3.4-5 ,[3] Genesis 3.6, [4] Deuteronomo 28.45,[5] Salimo 10.13, [6] Genesis 3.14-19, [7] Yesaya 59.2, [8] Cibvumbulutso 3.17, Aroma 3.10-18, [9] Genesis 3.15, [10] Mateyu 18.11, [11] Agalatiya 3.13, [12] Luke 1.26-38, [13] Luka 2.7, [14] Luka 2.8-12, [15] Luka 2.14, [16] Mateyu 2.9-11, [17] Mateyu 2.16, [18] Mateyu 1.21, Ezekieli 37.23, Hoseya 13.14, Agalatiya 4.5, [19] Aroma 3.23, [20] Yohane 3.3, [21] Yesaya 64.6, [22] 1 Timoteo 2.5, 1 Akorinto 1.30, [23] Ahebri 9.15, 1 Yohane 1.2, [24] Macitidwe a Atumwi 4.12, [25] Ahebri 4.15, 2 Akorinto 5.21, [26] Afilipi 2.4-8, [27] 1 Petro 3.18, [28] 1 Yohane 5.12, [29] Yesaya 45.22, [30] Marko 1.15, [31] Afilipi 3.20

bottom of page