top of page
Citonthozo cacikulu.png

CITONTHOZO CACIKULU

Kukwera Kumwamba kwa Yesu ndi kutumidwa kwa Mzimu wake Woyera

Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba – Luka 24.51


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi – Macitidwe a Atumwi 2.1


M’mudzi wina munali bambo amene anasamalira bwino ana ake asanu ndi awiri. Mkazi wake adamwalira ndiye ana anadalira pa iye. Anawakonda ndi kuwapatsa zonse zimene afunika kukhalabe ndi moyo. Dzina la bamboyo ndilo Mtendere.

Usiku wina Mtendere anauza ana ake kuti ayenera kuwasiya nthawi yaing’ono kuti awakonzere tsogolo labwino. Ana analira. Sanafune tate wao kupita cifukwa anamkonda. Mtendere anafotokoza kuti ayeneradi kupita koma analonjeza kuwasamalirabe. Tsiku lina anacokapo. Mitima ya ana inawawa kwambiri.

Patapita masiku ena anaona mwamuna amene anabwera ku nyumba yao. Anaoneka monga tate wao koma si iye: ndiye mbale wake. Anadza kuwasamalira mpaka tate wao atatsiriza kuwakonzera tsogolo latsopano. Kucokera tsiku ilo ana anamva bwino. Abambo anawakumbutsa lonjezo la tate wao. Ana anaphunzitsidwa za tate wao ndi makhalidwe ake ndipo analimbika pa kudziwa zina zambiri za iye. Anazindikira kuti tate wao ndiye munthu wodabwitsa ndi wosamalira ndipo sanaleke kuuza anzao zimene anamva za iye.

Kulibe munthu amene angafotokoze cimwemwe cimene cinaliko pamene tate anabwera kukayanjananso ndi ana ake.

~


M’Baibulo tiwerenga za Yesu amene anapita kukakonzekera ana ake malo Kumwamba. Anapatsa Mzimu wake Woyera kuwatonthoza ndi kuwaphunzitsa kuti akhale pa dziko lapansi ku ulemerero wa Mulungu. Iwo ayembekezera Yesu kubweranso ndiponso kuti adzakhala ndi Iye.


Mulungu ndiye M’modzi

Ndi cobvuta kumvetsa koma Mulungu akamba m’Mau ake, Baibulo, kuti Iye ndiye Mulungu m’modzi yekha komanso kuli Utatu Woyera wa Mulungu[1]: Mulungu Atate, Mulungu Mwana (Ambuye Yesu Kristu) ndi Mulungu Mzimu Woyera. Ndiwo amodzi: iwo onse ndiwo Mulungu, koma akhala ndi nchito zao zosiyanasiyana. Tiyenera kukhulupirira izi cifukwa Mulungu atiuza tero, ngakhale ndi cobvuta kuzimvetsetsa.


Yesu anakwera Kumwamba

Yesu, Mwana wa Mulungu, anacokera Kumwamba nabadwa pa dziko lapansi monga mwana[2]. Timakumbukira ici pa tsiku la Krismasi. Pa tsiku la Good Friday timakumbukira kuti anafa pa mtanda kupulumutsa ana ake ku cilango cifukwa ca chimo ndiponso ku imfa[3]. Patapita masiku atatu Yesu anauka kwa akufa[4]. Timakumbukira kuuka kwake pa tsiku la Paska.

Patapita kuuka kwake Yesu anadzionetsa ku anthu ambiri kuwasonyeza zoonadi za kuuka kwake[5]. Anawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Analangiza ophunzira ake kuyembekeza ku Yerusalemu mpaka alandira mphamvu ya Mulungu yowathandiza kulalikira za kulapa ndi kukhululukidwa ku macimo ku mitundu yonse[6]. Anawauza kuti sadere nkhawa cifukwa Iye ndiye wamphamvu yonse kumwamba ndi pa dziko lapansi ndiponso cifukwa sadzawasiya[7].

Masiku 40 anapitapo pamene Yesu anauka, pamene Yesu anali kulankhula ndi ophunzira ake, anawadalitsa nakwera kunka Kumwamba[8]. Sanaonekedwe cifukwa mtambo unamcotsa ku maso a anthu. Yesu anapita Kumwamba kukakhala pa dzanja lamanja la Atate ake[9]. Ndi kusiyana kwakukulu ndi zowawa ndi imfa zake zimene anali nazo pa dziko lapansi!

Yesu akhalabe Kumwamba. Ali ndi mphamvu zonse, ndiye wolemekezeka cifukwa ca nchito yopulumutsa imene anatsiriza ndipo alamulira.

YESU NDIYE MFUMU![10]

Ndi cofunikira kwambiri kwa anthu onse kukhala amodzi a Mfumuyu. Baibulo likamba kuti kulibe munthu amene ndiye mwana wa Mulungu mwa cilengedwe. Tiyenera kubadwa mwatsopano kukhala m’modzi wa Iye ndi kukhala m’Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kubadwa mwatsopano[11] cifukwa kulingana ndi Baibulo anthu onse ndiwo ocimwa[12] ndipo Mulungu akuda chimo. Cifukwa ca ici ocimwa saloledwa kukhala m’Ufumu wa Mulungu[13]. Chimo ndilo kusayeruzika[14]. Kuli macimo ambiri, mwacitsanzo kudzikweza, kusakhulupirira Mulungu, kuba ndi kucita cigololo kapena dama. Ngati sitilapa ndi kudalira pa Yesu pa cikhululukiro ca macimo athu[15], Iye si Mfumu wathu ndipo tiyenera kukhala ku Gehena nthawi zonse cifukwa ca macimo athu[16]. Gehena ndi malo oipa oposa kumene kuli zowawa, kukhala yekha ndipo kulibe ciyembekezo ciriconse[17]. Njira yeniyeni yopulumutsidwa ku Gehena ndi mwa Yesu[18].

Ngati mwabadwa mwatsopano ndipo mukhala m’Ufumu wa Mulungu muli ndi Mfumu Kumwamba amene alamulira moyo wanu ndipo akusamalirani[19]. Ngakhale zobvuta zithandizana kukucitirani ubwino. Zowawa zili gawo m’umoyo wa akristu ndipo mkati mwa kuyesedwa muli ndi Mfumu woyang’anira[20].

Patapita nthawi Yesu anakwera Kumwamba, angelo awiri anauza ophunzira kuti Yesu adzabweranso[21]. Kulibe munthu aliyense amene adziwa nthawi ya kubwera kwaciwiri kwake[22]. Angabwere nthawi iliyonse. Anthu onse adzamuona pamene adzadza[23]. Anthu onse (amoyo komanso akufa) adzaweruzidwa ndi Iye. Anthu ake adzakhala naye Kumwamba ku nthawi zonse, koma iwo amene sali ake adzakhala ku Gehena ku nthawi zonse pamodzi ndi Satana[24]. Yesu sanabwere cifukwa Mulungu afuna kuti anthu onse alape ndi kupulumuka[25], koma ciri comveka kuti ayandikira[26]


Kupatsidwa kwa Mzimu Woyera: tsiku la Pentekoste

Asanakwere Kumwamba Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti sadzawasiya nthawi iliyonse[27]. Komabe anakwera Kumwamba. Zoona, Yesu anasiya ophunzira ake m’thupi koma m’mzimu sanawasiye ndipo sadzasiya anthu ake onse[28]. Yesu anawalonjeza Mzimu wake Woyera kuwaphunzitsa ndi kutonthoza[29]. Mphamvu ya Mulungu Mzimu Woyera inaonekera m’njira yapadera masiku 10 patapita nthawi imene Yesu anakwera Kumwamba[30]. Tsiku ilo timacha ndilo tsiku la Pentekoste. Pa tsiku ilo Mzimu Woyera anadza m’nyumba m’mene ophunzira a Yesu anasonkhana. Ophunzira anaona ndi kumva zinthu zodabwitsa ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana kuti anthu onse anamva uthenga wa Mulungu m’cilankhulo cake: Yesu ndiye Mfumu. Anthu  ambiri analapa nakhulupirira Yesu ndiye Mpulumutsi wao[31]. Cifukwa ca mphamvu ya Mzimu Woyera ophunzira anayamba kucita zimene Yesu anawalangiza: kulalikira Uthenga Wabwino kwa mitundu yonse[32]. Anthu onse ayenera kumva Uthenga Wabwino: lapani, khulupirirani Yesu ndipo mudzapulumuka[33].

Mzimu Woyera agwirabe nchito. Mwa cisomo amaphunzitsa anthu za Yesu kuti amvetsetse kuti ayenera kulapa ndi kulandira Yesu monga Njira yeniyeni yopulumutsidwamo[34]. Kupulumutsa anthu otayika ndiko nchito ya Mulungu yekha[35]. Cifukwa ca ici kuli ciyembekezo ca munthu aliyense kuti apulumuke[36]. Macimo athu sakwaniritsa kutsutsa cisomo ca Mulungu kapena Mzimu Woyera kuti atiphunzitse ndi kudzindikiritsa za macimo, cilungamo ndi ciweruziro[37]. Ngakhale iwo amene samvetsa kuti afunika Yesu apulumutsidwe mwa mphamvu ya Mulungu.


Citanthauzo ca kukwera kwa Yesu Kumwamba ndi kupatsidwa kwa Mzimu Woyera m’masiku onse

Ngati inu si wopulumutsidwa ndi Yesu, kumbukirani kuti Yesu ndiye Mfumu wa dziko lonse lapansi. Tsiku lina adzabweranso ndipo mudzaweruzidwa ndi Iye. Umoyo wanu wonse udzavumbulutsidwa. Lapani ndipo mudzapulumuka ku Gehena[38]. Uzani Mulungu zonse zimene mufunika kupulumutsidwa nazo. Kulibe kalikonse komwe Mulungu sangagonjetse kuti mupulumuke. Iye ndiye wamphamvu ndi wofuna kukusinthani[39].

Ngati Yesu ndiye Mfumu wanu ndipo muli m’Ufumu wa Mulungu, kumbukirani kuti Mfumu wanu akusamalirani. Akupatsani Mzimu wake Woyera kutsogolera, kutonthoza ndi kuphunzitsa inu ndiponso kukukonzekeretsani ndi zipatso za uzimu[40]. Khalani moyo wanu kwa Iye ndipo osamcititsa cisoni mwa kucimwa[41]. Aloleni akutsogolereni kuti muphunzitse anthu ena Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu kuti adzapulumukenso ku ulemerero wa Mulungu.


~

Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu

Aroma 8.9b

--------------------

[1] Deuteronomo 6.4, Mateyu 28.19, [2] Luka 1.31, Luka 2.6-14, [3] Mateyu 27, [4] Mateyu 28, [5] Luka 24.31, 34 ndi 36, Yohane 20 ndi 21, [6] Macitidwe a Atumwi 1.3, Luka 24.49, Marko 16.15 ndi 16, Mateyu 28.19, [7] Mateyu 28.18 ndi 20, [8] Luka 24.50 ndi 51, Macitidwe 1.9, [9] Marko 16.19, [10] Cibvumbulutso 11.17, Cibvumbulutso 19.16, 1 Akorinto 15.25, [11] Yohane 3.5, [12] Aroma 3.23, [13] 1 Akorinto 6.9, [14] 1 Yohane 3.4, [15] Yohane 3.18, [16] Cibvumbulutso 21.8, [17] Mateyu 25.30, [18] Macitidwe a Atumwi 2.38, Yohane 5.24, Yohane 14.6, 1 Yohane 5.12, [19] Aroma 8.28, [20] Aroma 8.17, Afilipi 1.29, [21] Macitidwe a Atumwi 1.10 ndi 11, [22] Mateyu 24.36, [23] Cibvumbulutso 1.7, [24] Cibvumbulutso 20.12, 1 Atesalonika 4.16 ndi 17, Mateyu 25.31-46, [25] 2 Petro 3.9, [26] Mateyu 24, [27] Yohane 14.18, [28] Mateyu 28.20, [29] Yohane 14.16, Yohane 16.7, Yohane 14.26, [30] Macitidwe a Atumwi 2.1-13, [31] Macitidwe a Atumwi 2.41, [32] Marko 16.20, Macitidwe a Atumwi 11.20, Macitidwe a Atumwi 15.35, Macitidwe a Atumwi 28.31, Macitidwe a Atumwi 1.8, [33] Macitidwe a Atumwi 2.38, Macitidwe a Atumwi 16.31, [34] Macitidwe a Atumwi 16.14, Yohane 16.8, [35] Ezekieli 36.27, 1 Akorinto 6.11, Zekariya 12.10, [36] Yesaya 42.16, Yesaya 44.3, Marko 10.27, [37] Yohane 16.8, [38] Yesaya 45.22, [39] 1 Timoteo 2.4, Luka 13.34, [40] Agalatiya 5.22, [41] Aefeso 4.30

bottom of page