top of page
Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo, wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka – Salimo 103.8
Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndi nchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo – Aroma 11.6
Mabvuto ali m’ndende zaka zambiri. Patapita nthawi amasulidwa. Aganiza kuti apite ku banja lake. Asanafikeko ayenera kukhala usiku m’mudzi ndi anthu amene sadziwa. Alandiridwa bwino ndipo apatsidwa cakudya cabwino cimene anthuwo ali naco. Mabvuto sanadye cakudya cabwinoci zaka zambiri.
Dzuwa lalowa ndipo anthu onse agona. Koma Mabvuto sagona. Aganizira kuti awacitire ciwembu. Mwakacete-cete kwambiri ayamba kufuna-funa ndalama ndi zinthu zokwera mtengo m’nyumbamo. Aika zonse zomwe apeza m’cola cake cakutha ndipo acoka mobisala m’nyumba. Saonedwa ndi anthu.
Tsiku lotsatira Mabvuto atengedwa ndi apolisi ndipo abweretsedwa kwu anthuwo amene zinthu zao zinabedwa ndi Mabvuto. Ayembekeza kuti anthuwo adzakalipa kwambiri cifukwa iye anali wosayamika ndi woipa pa kuba za iwo ngakhale anamsamalira bwino.
Koma zonse zioneka m’njira ina monga Mabvuto aganizira. Anthuwo ndiwo acikondi ndipo ampatsanso cakudya cabwino kwambiri. Amfotokozera kuti sadzalola kuti apolisi amumange ndiye Mabvuto ayenera kumasulidwa. Ici ndi cinthu cotsutsana ndi cimene Mabvuto ayembekeza! Ayenera kuikidwanso m’ndende koma m’malo mwa ici amasulidwa! Mabvuto analandira cisomo: analandira cimene sanayenere.
M’Baibulo tiwerenganso za anthu amene analandira zimene sanayenere kulandira: m’Baibulo tiwerenga za cisomo.
Anthu onse ayenera kulangidwa
Colinga ca umoyo wa anthu onse ndico kukhala ku ulemerero wa Mulungu ndiponso kumtumikira ndi kumkonda. Koma m’Baibulo tiwerenga kuti anthu onse samvera Mulungu[1]. Kulibe wina aliyense amene amacita, amaganiza ndi kufuna zimene Mulungu alamulira ndipo anthu onse amacita, amaganiza ndi kufuna zomwe ziletsedwa ndi Mulungu. M’Baibulo kusamvera uku kuchedwa ‘chimo’. Ife tonse ndife ocimwa[2]. Baibulo likamba kuti aliyense yemwe acita chimo ndiye wolakwa ndipo ayenera kulangidwa[3].
Cilango ca ucimo ndi cakuti anthu atamwalira adzakhala ku Gehena[4]. Gehena ndi malo oipa koposa omwe tikhoza kufanizira, ndi malo omwe Satana adzakhala[5]. M’umoyo wathu zinthu zoipa zicitikanso cifukwa ca macimo[6], koma pamene Baibulo likamba za cilango cifukwa ca macimo cilango coipa coposa ndi kukhala ku Gehena nthawi zonse.
Mulungu ndiye wacifundo
M’Baibulo tiwerenga kuti sitikhoza kudzipulumutsa ku cilango ici coopsa ndi camuyaya[7]. Ngakhale timacita zinthu zabwino, sizidzathandiza kutipulumutsa[8]. Anthu ena amaganiza kuti adzaloledwa kukhala ndi Mulungu nthawi zonse m’malo mwa kukhala ku Gehena cifukwa amapita ku chalici kapena amawerenga Baibulo. Anthu ena amaganiza kuti macimo ao anakhululukidwa cifukwa anabatizidwa, amadya misa/mgonero kapena anakweza manja ao pamene munthu wina anafunsa, ‘Ndani amene akhulupirira Yesu?’ Anthu ena amanena kuti Mulungu adzawakhululukira cifukwa iwo amacita zotheka zonse kukhala m’njira yomwe Mulungu amafuna kuti azikhalamo. Koma Mulungu anena kuti tikalakwa pa lamulo lake limodzi ndiye kuti talakwira malamulo onse[9]. Kulibe munthu wopanda chimo. Ndiye si cothekadi kuti tingadzipulumutse ku cilango ca macimo athu.
Njira yeni-yeni yopulumukira ku macimo ndi cilango ca macimo ndi yakuti Mulungu atipatsa cisomo ndipo akhululukira macimo athu[10], monga m’citsanzo ca Mabvuto. Ngati macimo athu anakhululukidwa sitiyenera kulangidwa.
Baibulo likamba kuti Yesu anasenza cilango[11]!
Mulungu ndiye wacifundo kwambiri. Anatuma Mwana wake Yesu ku dziko lapansi. Yesu anacita zonse zimene zinali zofunikira kuti tipulumutsidwe ku cilango comwe tiyenera[12]. Yesu anazunzika ndipo anamwalira pa mtanda. Patapita masiku atatu anauka kwa akufa. Cifukwa ca ici tidziwadi kuti Yesu anasenza cilango conse ca macimo a anthu ake[13]. Uthenga wabwino womwe tiwerenga m’Baibulo ndi kuti ocimwa akhululukidwe ndi kulandira cisomo cifukwa ca nchito yaikulu yomwe Yesu anakwaniritsa[14]. Ocimwao adzakhalanso amodzi a anthu ake kwa iwo Yesu anasenza cilango ca ucimo.
Kupulumutsidwa mwa cisomo kupyolera mwa kukhulupirira mwa Yesu
Aliyense munthu ayenera kulandira cisomoco kuti apulumutsidwe ku cilango ca macimo ake. Mulungu amapatsa cisomo kwa iwo amene akhulupirira Yesu[15]. Mulungu atilamulira kukhulupirira Yesu. Kwinaku cikhulupiriro si cinthu cimene tiyenera kukwaniritsa koma cipatsidwanso ndi Mulungu mwa cisomo[16]. Ndiye Mulungu amapatsa zonse zimene tifunika kuti tipulumuke.
Kukhulupirira kutanthauza kukhulupirira zonse zomwe zalembedwa m’Baibulo[17]. Kukhulupirira kutanthauzanso kuika mtima wanu pa Mulungu, kuti akupulumutseni ku macimo anu cifukwa ca Yesu amene anazunzika ndipo anauka kwa akufa cifukwa ca macimo anu[18]. Kuthanthauzanso kubvomereza kuti kulibe njira ina yodzipulumutsa, koma kuti Mulungu amapatsa cikhululukiro mwa cisomo ndipo acotsa cilango[19].
M’Baibulo tiwerenga kuti ndi Mzimu Woyera amene amapatsa cikhulupiriro[20]. Amagwira nchito m’mitima ya ocimwa pa kugwiritsa nchito Baibulo[21]. Cifukwa ca ici ndi cofunikira kuwerenga Baibulo kawirikawiri ndiponso kumvetsetsa bwino pamene munthu wina awerenga Baibulo.
Kodi munalandira cisomo?
Ngati simunalandire cisomo muyenera kupempha Mulungu lero kuti akupatseni cisomo ndiponso kukhulupirira Yesu Uzani Mulungu macimo anu onse ndipo mfunseni kuti akhale wacifundo[22]. Osampempha kukhala wacifundo cifukwa ca ciriconse comwe mucita, koma cifukwa ca Yesu amene anafa pa mtanda ndi kuuka. Mulungu akulamulirani kumkhulupirira[23]. Werengani Baibulo masiku onse ndipo khulupirirani kuti Mulungu akhoza kukupatsani ciriconse comwe mufunika, cifukwa amapulumutsa ocimwa.
Ngati mudziwa kuti munalandira, yamikani Mulungu cifukwa ca zonse zomwe anakupatsani[24], angakhale munacimwa. Citani zimene Mulungu akufunsani m’Baibulo ndipo khalani moyo wanu ku ulemerero wa Mulungu[25].
~
Cisomo codabwitsaco
Capulumutsa ‘ne.
Woipa wopambanatu
Ndapeza moyo ‘ne.
Cisomoco cacotsadi
Mantha a imfayo
Pakukhulupirira ‘Ye,
Ambuye Yesuyo.
Cisomo candisungadi
Pa njira yangayo.
Cisomo cidzasunga ‘ne
Mpakatu kwathuko.
Kwathu ndidzayimba nyimbo
Ya cisomo cake,
Yolemekeza Mulunguyo
Ku nthawi zosatha.
~
Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi oyera mtima onse, Amen. – Cibvumbulutso 22.21
---------------
[1] Aroma 3.12, 1 Yohane 1.8 [2] Aroma 3.23 [3] Aroma 6.23, Eksodo 34.7 [4] Yohane 3.36 [5] Cibvumbulutso 20.10 [6] Aroma 8.20, Aroma 5.12, Mateyu 25.41 [7] Aroma 3.20 [8] Yesaya 64.6 [9] Yakobo 2.10 [10] Aroma 6.23, Aroma 3.24 [11] Yesaya 53.5 [12] 2 Akorinto 8.9 [13] Aroma 8.34, 1 Atesalonika 1.10 [14] Aefeso 2.4-8 [15] Aroma 3.28, Macitidwe a Atumwi 16.31 [16] Aefeso 2.5 ndi 8 [17] Yohane 17.17 [18] Aroma 5.1, Agalatiya 2.20 [19] Agalatiya 2.16 [20] 1 Akorinto 12.3 [21] 1 Akorinto 1.21, [22] Luka 18.13 [23] 1 Yohane 3.23, Macitidwe a Atumwi 16.31 [24] 2 Akorinto 9.15 [25] 2 Petro 3.18
bottom of page