Buku lapadera ndi umwayi wapadera
Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu – Aroma 10.17
Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima – Luka 18.1
Cifukwa ciani Baibulo ndi lofunikira?
Mulungu anatipatsa Buku lapadera. Bukuli ndi Baibulo. Baibulo linalembedwa ndi Mulungu yekha[1].
M’Baibulo tiwerenga zimene tiyenera kukhulupirira ndi kucita kuti tizikhala odalitsika m’umoyo wathu ndi kukakhala ndi Mulungu kumwamba pa nthawi zonse titamwalira[2]. Baibulo likamba kuti ici ndi cipulumutso. Kukhala obatizidwa, kudziwa kuturutsa ziwanda kapena kudziwa kulalikira sikukhoza kutipulumutsa ku Gehena. M’Baibulo tiwerenga za njira yeniyeni yopulumukiramo[3]. Cifukwa ca ici ndi cofunikira kwambiri kuwerenga Baibulo.
Kodi ndi ciani cimene calembedwa m’Baibulo?
M’Baibulo tiwerenga kuti anthu onse ndi ocimwa[4]. Ici citanthauza kuti munthu aliyense amacita, amaganiza ndiponso amafuna zomwe Mulungu aletsa. Citanthauzanso kuti aliyense samacita, samaganiza ndiponso samafuna zomwe Mulungu alamulira.
Ambuye Yesu anapereka citsanzo ca izi m’Baibulo. Kucita cigololo ndi cimo[5], koma Yesu ananena kuti kuyang’ana cabe mkazi (kapena mwamuna) ndi cimo ngati munthu afuna kuti mkaziyo (kapena mwamunayo) adzakhale wake[6]. Mulungu amadziwa zimene ziri m’mitima yathu[7]. Citsanzo cina cimene calembedwa m’Baibulo ndi kuti, kupha munthu ndi cimo, komanso kufuna kuti wina afe (kapena kuda wina) ndi cimo, cifukwa Mulungu amafuna kuti tizikonda anthu onse[8].
M’Baibulo tiwerenga Mulungu ndiye yani. Mulungu ndiye woyera[9]. Ici citanthauza kuti Mulungu ndi wabwino kwambiri ndiponso kuti alibe macimo. Mulungu amada macimo. Mulungu sakhoza kukhala pafupi ndi anthu cifukwa ndiwo ocimwa[10].
M’Baibulo tiwerenga kuti Mulungu ndiye cikondi[11]. Cifukwa ca ici anapeza njira kuti ubwenzi pakati pa Mulungu ndi ocimwa ubwererenso. Mulungu Atate anatuma Mwana wake Yesu ku dziko lapansi[12]. Yesu anafa pa mtanda cifukwa ca macimo a anthu ake, ndiye macimo ao onse anakhululukidwa[13].
Mungakhalenso wace kuti mupulumutsidwe ndiponso kuti ubwenzi pakati pa Mulungu ndi inu ubwererenso!
Baibulo limatiphunzitsa za njira yomwe Mulungu amafuna kuti tizikhala. Ndiye tikafuna kumtumikira ndi kumlemekeza m’umoyo wathu tiyenera kudziwa zimene zalembedwa m’Baibulo.
M’zirizonse zimene ticita tiyenera kucita zimene Mulungu atilangiza m’Baibulo[14], monga kulera ana, nchito, ndalama kapena chalici; nthawi zonse tiyenera kumvera Mulungu.
Kodi tiyenera kuwerenga bwanji Baibulo?
Anthu ena adzayankha kuti kuwerenga Baibulo ndi cobvuta. Ena adzayankha kuti alibe ndalama yogula Baibulo. Ngati muganiza motero mudzifunse: ‘Kodi Baibulo ndi lofunikira kwambiri kwa ine[15]?’ Kodi kuwerenga Baibulo sikuyenera kuyesetsa kwanu ndi ndalama zanu cifukwa kungalondolere cipulumutso? Siciri cotheka kuti mukondadi Mulungu koma simufuna kuwerenga Baibulo kuti mudziwe zina za Mulungu[16].
Pamene tiwerenga Baibulo tiyenera kupempha thandizo lake kuti timvetsetse zimene Mulungu atiuza. Kupempha Mulungu kapena kulankhula ndi Mulungu timacha kupemphera. M’Baibulo tiwerenga kuti ndi cofunikira kwambiri kupemphera[17].
Kupemphera ndiko kulankhula ndi Mulungu
Munthu amene samapemphera si Mkristu. Munthu amene amapemphera koma satanthauza zimene akamba si Mkristu. Pemphero limene likambidwa kopanda kuganizira si pemphero.
Cizindikiro ca Mkristu amene anapulumutsidwa ndi Mulungu ndi kuti amapemphera moonadi[18]. Anthu onse aloledwa kupemphera: Ana komanso anthu akulu-akulu, olemera ndi osauka, ophunzira ndi osaphunzira. Kupemphera ndi kuuza Mulungu zonse zimene ziri m’mitima yathu. Kupemphera ndi kuulula macimo athu[19]. Kupemphera ndi kufunsa Mulungu cikhululukiro. Kupemphera ndi kuyamika Mulungu cifukwa ca m’mene aliri ndiponso kumpempha Mzimu Woyera kuti tiziphunzira kukhala monga mwa cifuniro ca Mulungu.
Tingampemphenso madalitso koma tiyenera kuzindikira kuti colinga ca umoyo wathu ndi kutumikira Mulungu[20]; siciri kungokhala umoyo wabwino pamodzi ndi banja lathu ndi abwenzi athu ndiponso kopanda mabvuto a zacuma.
Tiyenera kupemphera modzicepetsa ndi mopereka ulemu cifukwa Mulungu ndi woyera[21]. Ndife anthu amene sitimamvera Mulungu masiku onse komabe tiloledwa kumpemphera. Ici ndi codabwitsa!
Kupemphera m’dzina la Yesu
M’Baibulo Mulungu alimbikitsa mitima yathu kuti tizipemphera[22]. Tiloledwa kupemphera m’dzina la Yesu. Ici citanthauza kuti Mulungu angayankhe mapemphero athu cifukwa ca kufa kwa Yesu pa mtanda.
Sitiyenera kucita cinthu cabwino ciriconse, kupemphera kwambiri kapena kupemphera pemphero lalitali kuti Mulungu atimvere[23]. Sitiyenera kupemphera kuti tidzayamikidwa ndi anthu[24]. Mulungu amadziwa zimene tisowa. Sitiyenera kufuulira Mulungu pamene tipemphera cifukwa Mulungu amatimva, ngakhale tilankhula motsitsa mau kapena tinena mosamveka kwambiri[25].
Cikhululukiro ca macimo, cipulumutso ndi ubwenzi watsopano ndi Mulungu ziri zotheka cifukwa ca Yesu yekha amene anafa pa mtanda ndipo anauka kwa akufa. Yesu ali ndi moyo ndipo amapemphera[26]. Tiloledwa kumpempha mobwereza-bwereza kuti azitikhululukire macimo athu. Ngati sitidziwa kupemphera, tingapemphere pemphero limene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake[27]. Ndi Mzimu Woyera amene amaphunzitsa pemphero lenileni m’njira imene Mulungu amafuna kuti tizipempherera[28].
Cilimbikitso
Iwo amene samawerenga Baibulo ndi kupemphera ali pa ciopsezo cacikulu. Moyo wao suonetsa kuti akonda Mulungu ndiponso kuti ndiwo Akristu, ngakhale anena kuti amkonda kapena ndiwo Akristu.
Werengani Baibulo lanu ndipo pempherani masiku onse[29]. Mucite izi mwaulemu, khalani odzicepetsa mtima ndipo citani izi mopirira ndi cilakolako kudziwa Mulungu. Werengani ndi kupemphera pamene muli nokha komanso pamodzi ndi banja lanu ndi ku chalici.
Kuwerenga Baibulo nthawi zambiri ndi kupemphera kwambiri ndi kofunikira kuti mumvetsetse zimene Mulungu akamba ndi zomwe akufunsani kuti mucite. Kuthandizanso kugonjetsa macimo.
Iwo amene amawerenga Baibulu ndipo amapemphera amatonthozedwa m’zocitika zirizonse[30]. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera ndi njira yolemekezera Mulungu! Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera kuyenera kukhala kofunikira koposa m’masiku onse a moyo wanu ndipo muzipirira[31], ngakhale simumvetsa zonse. Yamikani Mulungu kuti anatipatsa mphatso yapadera, Baibulo, ndiponso kuti atipatsa mpata kuti tingapite kwa Iye mwa pemphero.
Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m’cilungamo - 2 Timoteo 3.16
Nyimbo:
Werenga Baibulo lako pemphera tsiku lirilonse
pemphera tsiku lirilonse, pemphera tsiku lirilonse
Werenga Baibulo lako pemphera tsiku lirilonse ngati ufuna kukula
---------------
[1] 2 Timoteo 3.16, 2 Petro 1.21, [2] Yohane 3.18, [3] 2 Timoteo 3.15, [4] Aroma 3.10, 1 Yohane 3.10, [5] Eksodo 20.14, [6] Mateyu 5.27 ndi 28, [7] 1 Samueli 16.7, Ahebri 4.12, [8] Mateyu 22.39, [9] Yesaya 6.3, Yoswa 24.19, [10] Yesaya 59.2, [11] 1 Yohane 4.8, [12] Yohane 3.16, [13] Macitidwe a Atumwi 2.38, [14] Salimo 119.9, 2 Timoteo 3.16 ndi 17, [15] Salimo 1.2, [16] Salimo 11, [17] 1 Atesalonika 5.17, [18] 1 Petro 1.17, 1 Akorinto 1.2, [19] Danieli 9, [20] Aefeso 2.1-10, Mateyu 22.37-39, [21] Mlaliki 5.2, [22] Yohane 14.13 ndi 14, Salimo 81.10, [23] Mateyu 6.7 ndi 8, [24] Mateyu 6.5 ndi 6, [25] 1 Mafumu 18.21-39, 1 Samueli 1, Salimo 147.9, [26] Ahebri 7.25, [27] Mateyu 6.9-13, [28] Agalatiya 4.6, Zekariya 12.10, [29] Macitidwe a Atumwi 17.11, [30] Salimo 50.15, Afilipi 4.6 ndi 7, [31] Akolose 4.2