top of page
20220822_170628_2.jpg

BAIBULO LONSE

limalozera
Yesu Mpulumutsi

Yesu Mpulumutsi analonjezedwa, anabwera ndipo akhala Mfumu muyaya

Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uci m’kamwa mwanga – Salimo 119.103

Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu – Luka 4.21

Nthawi zambiri tikamba kuti Baibulo ndilo Buku lopatulika la Mulungu. M’kati mwa Baibulo tipeza mabuku ambiri. Mabuku awa pamodzi abvumbulutsa mwadongosolo ndondomeko ya Mulungu kotero kuti tikhoza kumvetsa momwe Mulungu ayanjananso ndi anthu ocimwa. Baibulo ndilo Buku lodabwitsa!

Mbali yoyamba ya m’Baibulo ichedwa Cipangano Cakale. Cisunga mabuku osiyanasiyana okwana 37 ocokera pa nthawi imene Yesu asanabadwe. Mbali ina ya m’Baibulo ichedwa Cipangano Catsopano. Mabuku a m’Cipangano Catsopano atiuza za kubadwa kwa Yesu, zimene zinacitika kucokera kwa nthawi iyo komanso zimene zidzacitika Yesu asanabwerenso.

Uthenga waukulu wa m’Baibulo m’Cipangano Cakale komanso m’Cipangano Catsopano ndi wa Yesu ndi nchito yake ya cipulumutso ya kubwezera anthu ocimwa m’ubwenzi wabwino ndi Mulungu mwa cisomo.


Cipangano Cakale: Yesu Mpulumutsi analonjezedwa

Mabuku a malamulo a Mulungu

Buku loyamba Genesis litiuza kuti Mulungu analenga zonse[1]. Cilengedwe ca Mulungu cinali cabwino koposa. Mulungu analenga Adamu m’cifanizo cace kukhala mutu wa umunthu[2]. Mulungu anauza kuti umunthu udzalandira umoyo wosatha Adamu akamvera Mulungu[3]. Sakanamvere Adamu, umunthu udzalandira imfa ya muyaya. Adamu sanamvere Mulungu[4]. Ici cinali tsoka! Tinagonja cifanizo ca Mulungu: sitikhalabe momwe Mulungu afuna ife kukhala. Ticimwa ndipo cifukwa cace sitikhozabe kulandira moyo wosatha mwa kumvera[5]. Posachedwapa kucimwa kwa Adamu, Mulungu analonjeza kutuma Yesu Mpulumutsi kugonjetsa chimo komanso kubwezera cifanizo ca Mulungu m’anthu ake ndi kuwapatsa moyo wosatha[6]. Lonjezo lodabwitsa mwa cisomo! Lonjezoli lipitiriza kuonekera m’mabuku ena a m’Cipangano Cakale.

Mulungu anasankha Abrahamu ndi ana ake (Aisrayeli) kukhala anthu ake[7]. Anawafuna kukhala omumvera kotero kuti mitundu ina idzaona mmene Mulungu aliri ndi kumkhulupirira. Komabe Satana mdani wa Mulungu anayesa mopitiriza kuononga Aisrayeli kuti Yesu asabadwe. M’Eksodo tiwerenga kuti Mulungu anapulumutsa Aisrayeli mwa cipsinjo ndiponso kuti anawatsogolera ku Kanani, Dziko la Malonjezano. Ici cinaonetsa kuti Mulungu ali wokhulupirika ndi wamphamvu. Mulungu anawapatsa malamulo kuwatsogolera m’mene ayenera kumtumikira. Tiwerenganso malamulo awa m’Levitiko, Numeri ndi Deuteronomo. Mwa malamulo awa a umoyo wa masiku onse ndi a cipembedzo cao, Aisrayeli anaphunzira kuti Mulungu sabvomera chimo lirilonse. Anaphunziranso kuti afunika Yesu wolonjezedwa kukhala Mpulumutsi wao kuti abwezeredwa m’cifanizo ca Mulungu[8]. 

Mabuku a mbiri

M’buku la Yoswa tiwerenga za Aisrayeli amene anagonjetsa Kanani, Dziko la Malonjezano. Komabe anaiwala Mulungu nalephera kukwaniritsa colinga cao ca kuonetsa anthu ena m’mene Mulungu aliri[9]. M’Oweruza, Rute, 1 ndi 2 Samueli, 1 ndi 2 Mafumu, 1 ndi 2 Mbiri, Ezara, Nehemiya ndi Estere tiwerenga momwe Aisrayeli anathana ndi adani ao. Nthawi zina Mulungu analola zobvuta kucitika monga njira ya kuwaitana kulapa macimo ao. Pamene Aisrayeli sanalape, iwo anatengedwa kapolo ku Babele dziko lacilendo. M’kati mwa kusamvera ndi kulangidwa kwa anthu, Mulungu anasunga lonjezo lake lakuti Yesu Mpulumutsi adzabadwa mwa iwo. Cifukwa cace Mulungu sanalole Aisrayeli kuthetsedwa.


Mabuku a nzeru

M’buku la Yobu tiwerenga momwe Yobu wanzeru anakhulupirira ndi kulemekeza Mulungu m’kati mwa zowawa[10]. M’buku la Masalimo tiwerenga nyimbo za anthu anzeru a Mulungu amene anaimba za ubwenzi wao ndi Mulungu m’zocitika zosiyanasiyana. M’nyimbo zao tiona cilakolako cao cakuti Mpulumutsi wolonjezedwa abwere[11]. M'mabuku a Miyambo ndi Mlaliki muli mau anzeru okhudza umoyo wa masiku onse. Buku la Nyimbo ya Solomon ligwiritsa nchito citsanzo ca ukwati kufotokozera cikondi ca Mulungu ca kwa anthu ake.


Mabuku a aneneri

M’mabuku a Yesaya, Yeremiya (amene analembanso buku la Maliro),  Ezekieli ndi Danieli tiwerenga mau a aneneri amene anachenjeza Aisrayeli pali macimo, aneneri onyenga, ansembe aciphupu ndi mafumu oipa. Anaphunzitsa kuti Mulungu afuna kuyanjananso ndi anthu ocimwa mwa Yesu Mpulumutsi wolonjezedwa amene adzabwera kusaukira ndi kufera anthu olapa ndi omkhulupirira. Anaphunzitsanso kuti Mulungu ali ndi mphamvu kucita tero[12].

Aneneri Hoseya, Amosi, Obadiya, Yona ndi Nahumu ananenera kwa anthu amene anasiya Mulungu. Ngakhale anthuwo anacimwa mopitirira, ciyembekezo cooneka pang’ono cipezeka m’mabuku awa: mwa cisomo Mulungu adzapulumutsa anthu, pakuti asunga lonjezo lake la kutuma Yesu Mpulumutsi. Mulungu ali wacifundo kwa iwo osayenera[13].

Aneneri Yoweli, Mika, Habakuku, Zefaniya, Hagai, Zekariya ndi Malaki ananenera makamaka za Yesu Mpulumutsi amene anali pafupi kubwera[14]. Analankhula za madalitso akulu cifukwa ca nchito yopulumutsa ya Yesu: anthu ambiri a m’dziko lonse lapansi adzayanjanitsidwa ndi Mulungu ndipo adzayamba kukhala momwe Mulungu afuna[15].


Cipangano Catsopano: Yesu Mpulumutsi wolonjezedwa anabwera

Mabuku a Uthenga Wabwino

Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane anali mboni ndi maso ya Yesu. Auza Uthenga Wabwino wa Yesu Mpulumutsi wolonjezedwa amene anabwera: Iye anabadwa monga mwana (Krisimasi)[16], anacita zodabwitsa, anaphunzitsa anthu, anafa pa mtanda (tsiku Lacisanu Loyera)[17], anauka kwa akufa (tsiku la Pasaka)[18] nabwerera Kumwamba (tsiku la kukwera kwa Yesu)[19]. Zonse zolembedwa m’Cipangano Cakale za Mpulumutsi zinakwaniritsidwa mwa Yesu komanso ndi Iye.

Buku la mbiri

Buku la Macitidwe a Atumwi litiuza kuti Yesu anatuma Mzimu wake Woyera (tsiku la Pentekoste)[20]. Anthu ambiri anakhulupirira Yesu Mpulumutsi cifukwa ca nchito ya Mzimu Woyera. Analalikira uthenga wa Yesu osati ku Israyeli (kwa Ayuda) cabe komanso kunja kwa dziko (anthu akunja kapena amitundu). Mzimu Woyera anatsogolera ndi kuthandiza anthu okhazikitsa mpingo wacikristu kotero kuti mpingowo unakula kungakhale mazunzo. Ufumu wa Mulungu unakula cifukwa ca nchito ya cipulumutso imene Yesu Mpulumutsi amene adabwera adacita[21].


Makalata

M’modzi wa okhulupirira Acikristu anali Paulo. Analemba makalata Aroma, 1 ndi 2 Akorinto, Agalatiya, Aefeso, Afilipi, Akolose, 1 ndi 2 Atesalonika kwa mipingo yacikristu yatsopano.

Makalata 1 ndi 2 Timoteo, Tito ndi Filemoni analembedwa kwa anthu pa okha. Colinga ca Paulo cinali kuthandiza Akristu kumvetsetsa bwino koposa za kubwezedwanso m’cifanizo ca Mulungu mwa Yesu Mpulumutsi amene adatha nchito yake ya cipulumutso[22]. Paulo analembanso za kukondweretsa Mulungu m’umoyo wa masiku onse ndiponso za kupangidwa kwa mipingo[23].

Wolemba kalata la Ahebri anawalitsa kuti Yesu Mpulumutsi adakwaniritsa Cipangano Cakale ndi malamulo a Mulungu[24]. Cifukwa cace okhulupirira acikristu sayenera kusunga malamulo a zocitika za m’cipembedzo ca Aisrayeli. Aliyense amene ali  mwa Yesu ayanjanitsidwa ndi Mulungu ndipo akhala ndi moyo wosatha mwa cisomo. Yakobo atsimikiza kuti cikhulupiriro cimayenda ndi nchito zabwino nthawi zonse[25]. Akristu sacita zabwino kuti apulumutsidwe, koma azicita mwa cikondi ca Mulungu monga cipatso ca kukhala opulumutsidwa.

M'makalata 1 ndi 2 Petro, 1, 2 ndi 3 Yohane ndi Yuda tiwerenga macenjezo a ciphunzitso ca bodza, taitanidwamo kukhala ndi moyo woyera ndiponso kuti tizikondana.


Buku la kunenera

Buku la Cibvumbulutso libvumbulutsa zoipa zambiri zimene zidzacitika Yesu asanabwerenso ku dziko lapansi. M’kati mwa mazunzo Mulungu asamalira anthu ake. Yesu akabwera ku dziko lapansi adzaweruza anthu onse. Iwo amene sali ake adzakhala ku Gehena muyayaya. Anthu ake adzakhala naye nthawi zonse kulemekeza Mulungu kaamba ka nchito yake yodabwitsa ya cipulumutso mwa Yesu amene analonjezedwa, anabwera ndipo akhala Mfumu muyaya.


Koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhala nao moyo m’dzina lace – Yohane 20.31

Baibulo lonse limalozera konse Yesu Mpulumutsi. Pemphani Mulungu thandizo lake pamene muwerenga Baibulo kuti muphunzire zina za Iye.


Cipangano Cakale: Yesu analonjezedwa

Kulengedwa -> Chimo -> Yesu Mpulumutsi analonjezedwa -> Mulungu anakumbukira lonjezo lake kungakhale kunali macimo ndi mabvuto -> Aneneri anaphunzitsa za Yesu Mpulumutsi amene anali pafupi kubwera

Cipangano Catsopano: Yesu anabwera

Kubadwa kwa Yesu -> Imfa ya Yesu -> Kuuka kwa Yesu -> Kupita Kumwamba kwa Yesu -> Yesu anatuma Mzimu wake Woyera -> Yesu anakulitsa mpingo wake mwa nchito ya Mzimu Woyera -> Akristu analembera okhulupirira makalata kuwalimbikitsa m’cikhulupiriro cacikristu -> Yesu adzabweranso kuweruza

bottom of page